

Mayi ndi mwana wake anapita kunkhalango.
Anapita kukathyola zipatso.
M'nkhalangomo, anapeza mtengo wa zipatso zakupsa.
Anagoneka pansi mwana wake amene anali mtulo, ndikukwera mumtengo.
Mlendo ochokera ku mudzi wina anadutsira pamene panali mwanayo. Ataona mwanayo, anali wodabwa.
Anadzifunsa yekha, "Mayi wake alikuti?"
Anawerama.
Phokoso la matcheni a m'khosi mwake linamudzutsa mwanayo.
Anamulola mwanayo kuti aseweretse matcheni akewo.
Mwanayo anasekelera posewerapo.
Mayi uja anayang'ana pansi kuti awone chimene mwanayo amasekerera.
Anaona munthu wachilendo.
Anali ndi mantha kotero anagwetsa chikwama chake cha zipatso.
Mlendoyo anayang'ana m'mwamba.
Ndipo anati, "Musaope, ndikungosewera ndi mwana wanu wokongolayu."
Kenako, mayiyo anatsika mumtengo muja.
Mlendoyo anatenga limodzi mwa matcheni akewo.
Anampatsa mwana uja, "Iyi ndi mphatso yako," anatero.
"Pitani kunyumba ndi mwana wanu. Mukawauze amuna anu akasamukire kumudzi wa mtendere. Mwana wanu wandipatsa mtendere," anatero mlendoyo.

