

Kalekale, kunali mwamuna wotchedwa Pempho ndi mkazi wake, Tilinawo.
Nthawi ya chilala, Pempho anachoka kwawo kukasaka ntchito. Pa nthawiyo, Tilinawo amayembekezera mwana wawo wa chiwiri.
Atakhala kutali kwa nthawi yayitali, Pempho anaganiza zobwelera kumudzi.
Asanayambe ulendo wawo, anapita kwa bambo wanzeru wokalamba kukafunsa malangizo.
Pempho atayilonjera nkhalambayo, iye anati, "Ndakhala kutali ndi kwathu komanso banja langa kwa nthawi yayitali. Tsopano ndikufuna kubwelera. Ndikufuna madalitso ndi malangizo anu."
"Mvetsera mwana wanga, pa ulendo wobwelera kwanu, osagwiritsa ntchito njira ya chidule. Osapereka ndemanga pa chilichonse chomwe wachiona. Osapanga chiganizo utakwiya," inalangiza motero nkhalambayo.
Pempho ananyamuka ulendo wake. Anakumana ndi amalonda anayi.
Atafika pa mphambano, amalondawo anasankha njira ya chidule. Potsata malangizo aja, Pempho anadutsa njira yayitali.
Amalonda omwe anadutsa njira yachiduleyo anaberedwa katundu ndi gulu la achifwamba.
Atayenda kwa tsiku lonse, Pempho anafika pa mudzi wina. Anapempha nyumba zambiri kuti agone nawo koma onse anamukana.
Bambo wina adati, "Sitilola alendo akhale m'nyumba zathu koma mukapemphe uko," adaloza nyumba ina.
Inali nyumba ya amfumu. Ambiri samachoka kunyumba imeneyi ndi moyo. Pempho anapita komweko. Ndapatsidwa chakudya chabwino ndi zakumwa.
Mkazi wa amfumu anali wokongola kwambiri.
Ataona nyumbayo, Pempho anafuna kufunsa kuti, "Kodi nyumba yanu mudayimanga bwanji?" Anafunanso kunena kuti, "Koma muli ndi mkazi wokongola amfumu!"
Koma anakumbukira zomwe nkhalamba ija inamulangiza ndipo anakhala chete usiku wonse.
M'mawa pamene Pempho amanyamuka, amfumu anamuitana.
"Aliyense amene amabwera m'nyumba mwanga amapereka ndemanga zokhudza nyumba komanso mkazi wanga. Inuyo simunatero, mukuyenera mwatumizidwa ndi Mulungu. Choncho ndikupatsani golide, chimanga ndi abulu," anatero amfumu aja.
Patatha masiku angapo, Pempho anafika kunyumba kwake. Anagogoda pa chitseko koma palibe amene anamutsekulira.
Atansuzumira polowetsera makiyi pa chitseko, adaona mkazi wake atagona ndi anyamata awiri. Adafuna kuwapha koma adakumbukira malangizo a nkhalamba ija.
Nkhalamba ija inamuuza Pempho, "Osapanga chiganizo utakwiya."
Patapita kanthawi, Tilinawo anatsekula chitseko ndipo anapeza mwamuna wake panjapo.
"Bwerani mudzaone abambo anu," Tilinawo anatero kwa ana awo awirirwo. Anasangalala pokumananso.
Pempho mothandizidwa ndi malangizo a nkhalamba ija, anapulumuka kwa achifwamba komanso kuphedwa ndipo anakhala wolemera.
Anakhala mosangalala ndi banja lake.

