

M'mudzi wina munali kusamvana pakati pa ogwira ntchito zosiyanasiyana.
Aliyense amaganiza kuti ntchito yake ndi yofunika kwambiri!
M'phunzitsi adati iye ndi ofunika kwambiri.
"Popanda aphunzitsi, simungapite ku sukulu kukaphunzira."
Womanga adati iye ndi wofunika kwambiri.
"Popanda womanga, simungakhale ndi sukulu zophunziliramo kapena nyumba zogonamo."
Kalipentala adati iye ndi wofunika kwambiri.
"Popanda makalipentala, mnyumba kapena sukulu zanu mukanakhala mopanda kanthu."
Dokotala adati iye ndi wofunika kwambiri.
"Popanda madokotala ndi anamwino, mukadadwala ndi kumwalira."
Mlimi adati iye ndi wofunika kwambiri.
"Popanda alimi, mukadakhala opanda chakudya."
Wophunzira adati iye ndi wofunika kwambiri.
"Popanda ophunzira, sikungakhale aphunzitsi, womanga, adokotala, alimi kapena makalipentala."
Pomaliza, aliyense adavomereza kuti ntchito zonse ndi zofunikira.
Timafuna aphunzitsi, womanga, madokotala, alimi, komanso makalipentala. Koma aliyense amayenera akhale wophunzira poyamba.

