

Tsiku lina, Akadeli, Luse, Akarati ndi Malia adapita kokathyola zipatso za m'tchire.
Adagwirana manja kuti awoloke mtsinje wawukulu.
Atsikanawa adapeza mtengo wa zipatso.
Adagwirizana zothyola zipatsozo atatseka maso awo.
Luse, Akarati ndi Malia sanatseke maso awo.
Akadeli yekha ndi amene adatseka maso ake.
Atatsekula maso awo, Akadeli yekha ndi amene adathyola zipatso zosapsa.
Luse, Akarati ndi Malia adamuseka Akadeli. Iwo adanyamuka ulendo wa kunyumba.
Akadeli adataya zipatso zosapsa zija ndipo adayamba kuthyola zakupsa.
Posakhalitsa, Akadeli adadzadza basiketi yake ndi zipatso zakupsa.
Adanyamuka payekha kukawoloka mtsinje waukulu uja.
Atafika pakatikati pa mtsinje, zipatso za Akadeli zinagwera m'madzi.
Adali wokwiya ndipo adayamba kulira.
Akadeli adaona nsomba yayikulu ndipo adaigwira.
Akadeli akuyenda kupita kunyumba, kamtema adatsomphola nsomba ija ndi kuuluka nayo.
Kamtemayo adagwetsa nthenga kuchokera ku chipsepse chake.
Akadeli adatola nthengayo ndikupitilira ulendo wa kunyumba.
Adakumana ndi gulu la ukwati. Ovina adavala udzu mmutu mwawo m'malo mwa nthenga monga mwa chikhalidwe.
Adatenga nthenga yake ndi kumupatsa ng'ombe yaikulu.
Akadeli adakafika kunyumba ndi ng'ombe yake. Makolo komanso abale ake adali okondwa kwambiri. Luse, Akarati ndi Malia adalakalaka sanamunamize Akadeli.
Linali tsiku la mwayi la Akadeli.

