

Kalekale, kudali mayi wina.
Iye amafunitsitsa atakhala ndi mwana.
Mayiyu adapeza dongo labwino.
Ndikuyamba kuumba mtsikana.
Mtsikana wowumbidwayo adasanduka munthu weniweni.
Mayiyu adamupatsa mtsikanayu dzina lotchedwa Kamdothi.
Mayiyu adali wokondwa kwambiri.
Adamukonda Kamdothi kwambiri.
Kamdothi adalangizidwa ndi mayi ake kuti asamatuluke mnyumba.
Kamdothi sanamvere. Nthawi zonse mayi ake akachokapo, Kamdothi anali kutuluka kukasewera ndi ana ena.
Tsiku lina, Kamdothi anali kunja kusewera ndi ana ena.
Kunayamba kugwa mvula yambiri.
Ana ena aja adathamangira ku nyumba zawo.
Pamene Kamdothi amathawa, miyendo yake idayamba kusungunuka. Adawerama ndi kubisala pakati pa zitsamba.
Ana ena aja adawauza makolo awo zomwe zidamuchitikira Kamdothi.
Anali okhumudwa komanso odabwa.
Mayi uja atamva zomwe zidamuchitikira Kamdothi, adalira kwa masiku ambiri.
Anthu am'mudzi adatenga mtsikana wamasiye kuti alowe m'malo mwa Kamdothi uja.
Koma sizidali zofunika Chodabwitsa chachikulu chinali kumudikira mayi uja!
Usiku wina, panamveka kugogoda pa chitseko.
"Kodi angakhale ndani?" adadabwa mayiyu.
Kamdothi adabwera kunyumba.
Adali wotopa komanso wodwalika.
Mayi ake adagulitsa katundu wawo yense. Ndalamazo adagwiritsa ntchito kumupitisa Kamdothi kuchipatala.
Kamdothi adakula ndi kukhala mtsikana wokongola kwambiri.

