

Kariza anali kukonda kufunsa mafunso. Iye anatenga khalidwe limeneli kucokera kwa makolo ake.
Iwo amanena kuti, "Ngati sufunsa mafunso pomwe uli wam'ng'ono, udzakula uli wacikulire wopanda nzeru!"
Tsiku lina, Kariza anafunsa aphunzitsi ake kuti, "N'cifukwa ciyani makolo athu amatiuza kusamba m'manja nthawi zonse pomwe tisanayambe kudya, ngakhale kuti manja athu awoneka oyera?"
Aphunzi anzake analikonda funso lake. Nawonso sanakonde kuuzidwa kusamba m'manja.
M'phunzitsi anayankha nati, "Kariza limenelo ndi funso labwino. Ngakhale pamene manja athu akuwoneka oyera, iwo angakhale ndi tizilombo."
M'phunzitsi analongosola, "Tizilombo timayambitsa matenda. Sitingawone tizilombo timeneti pogwiritsa nchito maso athu, timafunikira cinthu cinacake camphamvu kwambiri cowonera tizilombo."
Aphunzitsi anatenga maikrosikopo kucokera mu kabati. "Maikrosikopo ndi ndi ciwiya cogwiritsa nchito kuwonera zinthu zocepa kupenya ndi maso athu aumunthu," iwo anatero.
Mofulumira aphunzitsi anakwengula manja a Kariza ndi kamtengo ndipo pambuyo pake anapukutira dothi limenelo pa kagalasi ka maikrosikopo.
Aphunzitsi anayika kagalasi pa maikrosikopo ndipo izi ndi zomwe anaona popenyera.
Ngakhale kuti manja a Kariza sanali kuwoneka ndi dothi, munali tizilombo m'manja akewo.
"Pali tizilombo pa malo aliwonse otizungulira, pa zinthu zomwe timagwira m'kalasi, panja pabwalo losewerera kapena kunyumba.
Tizilombo timeneti tingatidwalitse kwambiri ife," anacenjeza tero aphunzitsi.
Iwo anapitiriza, "Kuti tiphe tizilombo timeneti, tifunikira kusamba m'manja ndi sopo ndi madzi abwino, makamaka pomwe tisanayambe kudya.
Ndipo pamene tadwala tiyenera kusamba m'manja kotero kuti tisafalitse tizilombo timeneti."
Pamene anafika kunyumba, Kariza anapeza atate ake akupanga kaciwiya kocititsa cidwi. ''Kodi mukupanga ciyani?'' iye anafunsa.
"Cimeneci cichedwa kuti 'imirira ndi kusamba'," anatero atate ake. "Ungakagwiritse nchito kusamba m'manja pambuyo pogwiritsa nchito cimbudzi, ndi pambuyo pa cakudya ciliconse."
Kariza anadabwa ndipo anati, "Inde zoonadi! Aphunzitsi athu anatiuza za ciwiya cimeneci, koma ambirife sitimadziwa mocigwiritsira nchito. Kodi cimagwira nchito bwanji?"
Atate ake anaseka ndipo anamuuza kuti, "Bwera pafupi ndipo ndidzakuwonetsa, mwana wanga."
"Coyamba, ponda pa cidutswa cathabwa pansipa," anatero atate ake.
"Pambuyo pake ciwiya camadzi cidzapendeka ndi kuthira madzi pamanja ako.
Kumbukira kusambira ndi sopo," iwo anamuuza Kariza.
Kariza anakondwera ndipo anati, "Kodi ndikanadziwa bwanji cimeneci popanda kufunsa mafunso?
N'zoona kuti mafunso amatsogolera ku cidziwitso."

