

Tsiku lina, amayi anagula zipatso zosiyanasiyana.
"Kodi ndi liti pomwe tingadye zipatso?" tinawafunsa.
"Tidzadya zipatso usiku uno," anayankha amayi.
M'bale wanga Musonda ndi womana.
Analawa zipatso zonse. Iye anadya zambiri.
"Onani zimene Musonda wacita," anatero m'bale wanga wamng'ono.
"Musonda ndi wosamvera ndipo ndi wodzikonda," ndinatero ine.
Amayi anakwiya ndi zimene anacita Musonda.
Ife tonse tinakwiya ndi zimene Musonda anacita.
Koma Musonda sanamve cisoni.
"Kodi mudzamulanga Musonda?" anafunsa m'bale wanga wamng'ono.
"Musonda, udzamva cisoni posacedwapa,'' anacenjeza amayi.
Musonda anayamba kusamva bwino.
"M'mimba mwanga muwawa,'' anatero Musonda motsitsa mawu.
Amayi anadziwa cifukwa cake Musonda anali wodwala.
"Zipatso zikumulanga Musonda,'' anaganiza tero amayi.
Pambuyo pake, Musonda anapepesa kwa ife. "Sindidzakhalanso waumbombo," analonjeza.
Ife tinamukhulupirira.

