Kalekale, panali anyamata awiri amene ng'ombe zawo zinasowa.
Anazinyang'ana ng'ombezo mpaka kunawadera.
Pamene mdima umagwa, anaona kuwala mnyumba ina.
Anagwirizana zokapempha malo ogona.
Anapita ku nyumba ija ndi kugogoda. Chitseko chinatsekulidwa ndipo analowa.
Anyamata aja sanaone wina aliyense. Koma anamva mawu akuwapatsa moni.
Mawuwo anati, "Ndine nsabwe. Vundukulani poto mutengemo chakudya. Vundukulani m'phikawo ndipo mumwe thobwa lili m'menemo."
Kenako nsabwe inavala chikopa chake ndikupita panja.
Anyamata aja anadya, anamwa ndi kuthokoza.
Kenako anatuluka m'nyumba muja.
Atanyamuka, anayamba kuganiza zoipa. Anati, "Ayi, sitimayenera kudya chakudya cha mnyumba ya nsabwe."
Ndipo anaganiza zobwereranso kunyumba kuja ndi kukaithudzula nsabwe ija.
Anabwereradi kunyumba kuja ndi kukaithudzula nsabwe.
Mwadzidzi nsabwe ija inasowa, ndipo nyumba ijanso inasowapo!
Anazindikira ali panja popanda nyumba.