

Tsiku lina, Nanzikambe anamuuza Kalulu kuti achite mpikisano othamanga kuti adziwe amene amathamanga kwambiri.
Kalulu anavomera ndipo anati, "Iwe umayenda pang'onopang'ono! Umayamba ndi mwendo umodzi, kenako wina, kudzayambiranso ndi wina uja."
Kalulu anadzitukumula, "Ndikusiya kumbuyo kwambiri. Sungandipezenso!"
Anaitana nyama zina zonse kuti zidzawonerere mpikisano uja.
Nanzikambe ndi Kalulu anaima pa mzere kudikira kuti ayambitse mpikisano uja.
Mpikisano utayambika, Nanzikambe anajowera pa mchira wa Kalulu.
Nyama zina zija zinaseka kwambiri.
Kalulu sanadziwe kuti Nanzikambe anali pa mchira wake.
Kamba komva phokoso lija, Kalulu anayima mwadzidzi. Nanzikambe anadumpha kuchoka pa mchira wa Kalulu uja.
"Iwe! Uziona kumene ukupita! Ukuchedwatu," Nanzikambe anamukuwira Kalulu.
Kalulu anadabwa. Anayambiranso kuthamanga.
Samadziwa kuti Nanzikambe wajoweranso pa mchira wake.
Mmene Kalulu amayandikira pothera mpikisano, nyama zina zija zinaona kuti Nanzikambe anali pa mchira wa Kalulu ujabe. Nyama zina zija zinaombera mmanja ndi kuseka.
Kalulu anamvanso phokoso ndipo anaganiza kuti Nanzikambe wafika kale pomalizira mpikisano.
Atafika pomalizira mpikisano, Nanzikambe anajowapo pa mchira wa Kalulu.
"Bwino ungandiponde! Ndayamba ndine kufika!" Nanzikambe anamukalipira Kalulu uja.
Kalulu anachoka ndi ukali.
Nanzikambe anatsalira kulandira mphotho, ndipo Kalulu sanapambane mpikisano uja.

