

Dzuwa limatuluka m'mawa, kuchokera ku m'mawa.
Ndimamva tambala akulira mbandakucha.
Dzuwa limadutsa pamwamba pa nyumba ya Tefa, chakudya cham'mawa tisanadye.
Ndimamva kununkhira kwa tiyi ndi zitumbuwa kutsatira kuwala kwadzuwa pa windo langa.
Dzuwa limapita kuseli kwa mitengo masana kusukulu.
Kenako limafika pa madzi odikha pakati pa bwalo losewererapo.
Dzuwa limayima pamwamba pa mutu wanga. Chithunzithunzi changa chimakhala pambali panga.
Timasewera masewero a chithunzithunzi ndi anzanga.
Chithunzithunzi changa chimakula, kenako kuchepa. Timachithamangitsa.
Chithunzithunzi changa chimatalika, kenako kufupika. Timachithamangitsa.
Ndimaima, anzanganso amaima. Timaona zithunzithunzi zathu zikuvina.
Timatopa kenako ndikubwereranso mkalasi. Tikaweruka timapita kunyumba.
Dzuwa limayasamula.
Ndimaliona dzuwa likuzimirira kumadzulo. Ndimaona chithunzithunzi changa pa khoma.
Ndi nthawi yokagona.
Dzuwa limatsika kuseli kwa mitambo.
Ndimagona pabedi panga, ndipo ndimalota dzuwa likupita kutali kwambiri.

