Popi agwa
Salome Ledwaba
Martin Letsoalo

Uyu ndi galu wanga. Dzina lake ndi Popi.

Iye ndi galu wosaka.

1

Popi amakonda kusaka nyama zazing'onozing'ono.

Amakondanso kusewera mu udzu wautali.

2

Loweruka lina, Popi adapita kokasaka yekha.

Iye anaona kalulu ali pa mwala.

M'kamwa mwa Popi munakha dovu.

3

Kalulu anaona Popi akumuyang'ana.

Kalulu anathawa mwaliwiro.

4

Popi anamuthamangitsa kalulu uja.

Iye ankangoganizira zomudya Kaluluyu.

Sanaone kuti kutsogolo kwake kunali dzenje lalikulu kwambiri.

5

Popi anagwera m'dzenje lozama lija.

Kalulu anathawa molizungulira dzenjelo ndi kupitilira kuthawa.

6

Mwamwayi, anyamata awiri anamva Popi akuwuwa "Wuu! Wuu! wuu!"

Iwo anathamangira ku dzenje lija kukamuthandiza Popi.

7

"Ndiwolemera kwambiri" anadandaula anyamatawo!

Koma anakwanitsa kumutulutsa Popi m'dzenje muja.

Anali galu wokondwa kwambiri.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Popi agwa
Author - Salome Ledwaba
Translation - Peter Msaka
Illustration - Martin Letsoalo
Language - ChiChewa
Level - First sentences