Nyerere anali mlimi wabwino. Amakhala m'nthaka ndi banja lake.
Amagwira ntchito molimbika pa munda wawo. Banja la nyerere limakhala bwino.
Nkhunda anali neba wa Nyerere. Banja la Nkhunda limakhala mumtengo.
Nkhunda ndi banja lake samalima. Amapumula tsiku lonse.
Nkhunda ndi banja lake amayimba bwino kwambiri.
"Tigawireni chakudya?" Nkhunda inapempha. "Ayi! Mukalime zanu!"
Nkhunda inawulukira pansi ndikuyamba kuyimba, "Nyerere ndi mfumu!"
"Nyerere ndi mfumu! Nyerere ndi mfumu!" Nyerere inasangalala ndi nyimboyi.
Atamaliza kudya, Nkhunda ndi banja lake anawulukiranso mumtengo wawo uja.
Tsiku linalo, Nkhunda inaseka Nyerere. "Mafumu amakhala ndi mutu waukulu?"
"Ndiwe osayamika komanso waulesi!" inadandaula motero Nyerere.
"Pepa!" inatero Nkhunda, ndipo inayamba kuyimba, "Nyerere ndi mfumu!"