Mwana wa Udzudzu
Peter Lebuso Boase
Peter Lebuso Boase

Kalekale, nyama zonse zimayankhula.

Mayi Udzudzu ndi mwana wake amakhala mnyumba.

1

Mayi Udzudzu amamusiya mwana wake kunyumba akamapita kokasaka zakudya.

2

Tsiku lina, Mayi uja atachoka pakhomo, Mwana wake anapita panja.

3

Mayi Udzudzu atabwera, anapeza kuti mwana uja wapita panja.

4

Mayi Udzudzu anada nkhawa. Mwana wake anali kunja yekha.

Posakhalitsa, mwana uja anatulukira.

5

Mwana uja anali okondwa kwambiri.

"Amayi, anthu anali okondwa kwambiri kundiona. Amandiombera m'manja nthawi zonse ndikamawadutsa ndikuuluka!"

6

Mayi Udzudzu uja anachita mantha.

"Ukuti anthu anali okondwa ndi iwe ndipo amakuimbira m'manja?" Anamufunsa mwana uja.

7

"Sanali okondwa kukuona iwe. Amafuna akuphulitse!" Anafotokoza mayi uja.

"Anthu sakondwa akaona udzudzu," anamuchenjeza.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mwana wa Udzudzu
Author - Peter Lebuso Boase
Translation - Peter Msaka
Illustration - Peter Lebuso Boase
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs