

Kalekale, kunali fulu wina dzina lake Likhutu. Likhutu amakhala pafupi ndi msika.
Pamsikawu, panali mayi wina amene amaphika ndi kugulitsa mandazi. Anthu ambiri amaima pamzere kugula mandaziwo.
Likhutu anatengeka ndi kununkhira kwa mandaziwo. Amafuna atagulako.
Tsiku lina, Likhutu anapita kwa mayi ogulitsa mandazi uja. "Pali ganyu yoti ndigwire kuti mundilipire mandazi?" Anafunsa Likhutu.
"Eya, uzindiyang'anira sitolo yangayi ndikupita ku Gulu la Amayi la Chama," anayankha motero mayi aja.
Mayi aja atachoka, Likhutu anatengeka ndi kununkhira kwa mandazi.
Anayankhula mumtima, "Ndidya mandazi mmene ndingathere. Ndipo ndisungako ena muchipewa changachi."
Asanamalize kudziyankhulira anaona mayi wa mandazi uja akubwera potelopo.
Anachinyira mandazi ochoka kumene pamoto muchipewa chake.
Kenako anavindikira chipewa chija m'mutu mwake. Pompopompo, Likhutu anayamba kuzunguza khosi lake kamba ka kuotcha kwa mandazi.
Mayi aja atafika, anadabwa kumuona Likhutu akuzunguza khosi lake mwamphamvu.
Anafunsa, "Chilipo chikukuvuta?"
"Palibe chikundivuta!" anayankha Likhutu.
Anathamanga kupita kunyumba ya msuweni wake.
Anapeza msuweni wake akucheza ndi alendo, kotero anakhala panja ndikumadikira.
Likhuthu anapitiriza kuzunguza khosi lake pamene amadikira.
Msuweni wake ataona Likhutu akuzunguza khosi lake, anadabwa.
Ananyamuka msanga ndi kukoka chipewa cha Likhutu. Mandazi aja anagwa pansi.
Tsitsi lonse la Likhutu linali litapsa. Tsopano anali ndi dazi.
"Chakuchitikira ndi chiyani?" anafunsa msuweni wake uja. Koma Likhutu anasowa choyankha kamba ka manyazi.
Tsitsi la Likhutu silinamelenso.
Kuchokera nthawi imeneyo, afulu onse alibe tsitsi.

