

Kalekale, afisi anavutika ndi njala. Chifukwa cha chilala, ngakhale mbuzi, mberere ndi ng'ombe zinasamukira kwina. Afisi analibiletu chakudya.
Anasonkhana pa malo amodzi kuti akambirane za vutoli.
M'modzi wa afisi aja anati, "Mwachikhalidwe chathu, ife timadya chilichonse chimene chikuthawa. Taonani, mitambo iyi ikuthawa."
Fisiyu anakhulipirira kuti mitambo imathawira ku malo ena. Anati, "Tiyeni tiidye."
Pompo, afisi onse anayang'ana kumwamba ndipo anaona mitambo ikuyenda mlengalenga.
M'modzi mwa afisi ang'ono kwambiri anafunsa, "Ndiye tingaigwire bwanji mitambo? Ili kutali kwambiri ndi pansi pano."
Fisi wamkulu kwambiri anati, "Fisi wamphamvu kwambiri aime pansi ndipo ena tonse tikwere ndi kuima pamsana pa wina aliyense mpaka titafikira kumitambo."
Anagwirizana ndipo anayamba kukwerana pamsana.
Posakhalitsa, pansi siipanatsalenso fisi kupatula wamphamvu uja.
Afisi ena onse aja atakwera, fisi anali pansi uja anaganiza kuti anzake ayamba kudya.
"Ndi chifukwa chiyani simukundigairako chakudya chimene mukudya?" Anafunsa motero.
Koma, afisi aja sanafikire mitambo ija.
Sanapezenso chakudya chilichonse, kotero analibe choti amupatse fisi wamphamvu amene anaima pansi uja.
Fisi wamphamvu uja ananyanyala ndipo anasunthira kumazere. Afisi ena onse aja anagwera mbali ya kumanja.
Pachifukwa icho, afisi onse lero amatsimphina mbali ya kumanja.

