

Abike anagona pamphasa. Amamvetsera imodzi mwa nkhani za kumtima kwake imene mayi ake amamufotokozera.
Nkhani inali yokhudza amayi a m'mudzi mwawo amene amadziwika ndi kupanga mikeka ndi madengu zokongola.
Mphatso ya pamtima ya Abike inali mkeka ogonapo omwe agogo ake akazi anamupangira atakwanitsa zaka khumi.
Abike atadzuka, amayi ake amafuna kupinda mkeka uja. "Dikirani amayi, tiyeni tione makaka ndi zojambulazi limodzi," Abike anatero.
Abike anatchula mitundu ya mizere, kuchokera m'munsi mpaka m'mwamba, "Pinki, pinki, wobiriwira, wobiriwira, buluu, buluu, pinki, pinki, wobiriwira, wobiriwira."
Mungaone pamene kalukidwe kakusintha pa mkekawu?
Abike anautambasula mkeka uja. Zojambula zambiri zinali za makona anayi, ndipo zina zinali zofanana mbali zonse zinayi. "Ndimadziwa njira yachidule yowerengera kuti zojambula zonse zilipo zingati," Abike anatero. "Sitiwerenga chojambula chilichonse pachokha, timangowerenga kuti pamzere zilipo zingati."
Mukudziwa m'mene Abike amawerengera zojambula?
Zilipo zingati zonse?
Abike analinso ndi mkeka wina waung'ono umene amakhalapo akakhala panja.
Mkeka umenewu unali ndi zojambula za mbali zinayi. Nanga Abike wakhala pa zojambula zingati? Nanga ndi zojambula zingati zimene sizinakhalilidwe?
Kodi mungagwiritse ntchito njira ya chidule ya Abike yowerengera zojambula zonse zili pa mkekawu?
M'mawa wa tsiku lina Abike anapita kukayendera agogo ake a akazi. Pachitsime, anaona akazi akutunga madzi ndi mabigiri amene amasenza pamutu pawo.
Iye anadzifunsa, "Kodi bigiri imodzi inganyamule madzi okwana malita angati?" Inu mukuganiza bwanji?
Abike anafika kunyumba ya agogo ake. "Waganiza bwino kundiyendera Abike! Taona dengu ili limene ndangopanga kumene. Ukuliona bwanji?" Agogo anafunsa.
"Mitundu yake yandisangalatsa, koma zonjambulazi zili ndi nsonga zosongoka kwambiri," anayankha Abike. Kodi mungakopere bwanji maonekedwe a zomwe zili pa basiketi?
Nanga zojambulazi zili ngati chiyani, zambali zinayi zofanana kapena zofanana mbali ziwiri zokha kapena ndi za maonekedwe ena?
Pa ulendo wake obwerera kumudzi, Abike anasochera. Samadziwa kumene anali, kotero anakhala pansi pa mtengo kuti apume.
Abike anaonetsetsa masamba a mitengo akuvinavina munthambi. Kuwala ndi mthunzi zimalowana bwino pamalo onsewo. Posakhalitsa, anagona tulo tofa nato.
Atadzuka, anachita mantha. Amafuna ali ndi mayi ake kunyumba, akupumula pa mkeka wake.
Nthawi yomweyo, kambalame ka mtundu wa buluu kanatera pamtengo. "Uli bwanji? Osadandaula, nditha kukuthandiza kubwerera kunyumba. Nditsatire," kanayankhula moyimba.
Abike anadabwa kumva mbalame ikuyankhula.
Abike anaitsatira mbalame ija mosavuta mpaka anafika pa mphambano. Njira inagawanikana pawiri, ina imapita kumazere ina kumanja. Kodi atenge njira iti?
Abike anapenya m'mwamba. Zatheka bwanji? Mbalame inali ndi kachidutswa ka mkeka wake kukamwa kwake.
Inawuluka m'mwamba mwa njira ya kudzanja la manja ndi kugwetsa kachidutswa ka mkeka. Kenako inawuluka kumapita.
Abike anatsatira njira yopita kumunsi kwa phiri.
Anamva kuseka ndi kuimba kwa anthu a m'mudzi wa kwawo. Abike anali okondwa kufika kunyumba.
Amayi ake anamuyalira mkeka wake ndi kumupatsa chakudya kuti adye.
Abike anayamba kuwerenga zojambula kuti atsimikize kuti zonse zinalipo. Akuwerenga anaona kachidutswa kamene kanatengedwa koma ndi kubwezeredwaponso.
Kotero, iye sanali kulota. Kambalame kabuluu kaja kanali kenikeni!

