Abebe ndi anyamata a Chizungu
Kokeb Abera
Adonay Gebru

Abebe anali mkalasi yake yoyamba ya sukulu.

Abambo ake anali mlimi. Chaka china, abambo ake a Abebe anadzala tirigu m'munda mwawo.

Tsiku ndi tsiku akachoka kusukulu, Abebe amapita kumunda kukathandiza bambo ake.

1

Pafupi ndi munda wa tirigu uja panali bwalo la masewera a mpira wa miyendo. Tsiku lina masana Abebe akuthamangitsa mbalame, anyamata anayi a chizungu anabwera kudzasewera mpira.

Anyamata aja anayamba kusewera. Mpira unanjanja ndikugwera m'munda wa tirigu uja.

2

Mpira uja unawononga tirigu wina. M'modzi wa anyamata aja anathamangira m'munda muja kukatola mpira, ndipo anawononganso tirigu wina.

Anapitiliza kusewera mpira. Mpira uja unanjanjanso ndi kugweranso m'munda muja kambirimbiri.

3

Anyamata aja anapitiliza kukatola mpira m'munda muja. Ulendo uliwonse amawononga tirigu uja.

Abebe ndi bambo ake anakwiya kwambiri kamba ka kuwonongeka kwa mbewu zawo.

4

Abebe ndi bambo ake, onse samatha kuyankhula Chizungu. Samadziwa kuti anganene bwanji kuti, "Osalowa m'munda. Lekani kuwononga mbewu zathu!"

Anyamata a Chizungu aja samadziwanso chiyankhulo china kupatula Chizungu.

5

Abambo a Abebe anati, "Mwana wanga, gwiritsa ntchito zimene unaphunzira kusukulu. Awuze asiye kuponyera mpira m'munda mwathu!"

Nthawi imeneyo n'kuti Abebe anangophunzira zilembo za chizungu A, B, C, D, E, F basi.

6

Abebe anafuna kuwakalipira anyamata aja. Koma samadziwa kunena kwake mchizungu.

Mpira unanjanjiranso m'munda wa tirigu uja. Mnyamata m'modzi anathamangira mpira uja mpaka m'munda.

7

Abebe anathamangira kumene kunali mnyamata uja, akukweza manja ake m'mwamba. Anayamba kukuwa. Anakuwa mokweza kwambiri komanso momveka bwino, "A, B, C, D, E, F!"

Anakuwa katatu "A, B, C, D, E, F!"

8

Mnyamata wa chizungu uja anasiya kuthamangira m'munda wa tirigu uja. Anzake anali m'bwalo la mpira aja nawonso anangoima ndi kumayang'ana Abebe.

Kenako anayamba kuyankhulitsana okhaokha m'chizungu ndikuyamba kumwetulira. Anadziwa zimene Abebe amafuna kunena.

9

Mnyamata amene anakatola mpira uja anayenda mosamala m'munda wa tirigu uja.

Kenako anyamata anayi a chizungu aja anapita kukasewerera kutali ndi munda uja.

Abambo ake a Abebe anadabwa. Anakhulupilira kuti mwana wawo anayankhula Chizungu.

10

Abambo anati, "Aah, mwana wanga, ndiwe wolimba mtima komanso wochenjera!" Anamunyadira kwambiri mwana wawo.

Abebe naye analinso odabwa komanso okondwa. Anasowa chonena.

11

Abambo a Abebe anamulimbikitsa sukulu, komanso kuti apitilize maphunziro ake.

Abebe anaphunzira ziyankhulo zitatu ndipo anazidziwa bwino kwambiri. Anakhala ogwira ntchito yotanthauzira ziyankhulo komanso mlembi.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Abebe ndi anyamata a Chizungu
Author - Kokeb Abera, Mohammed Mesele, Tibebu Tadesse
Translation - Peter Msaka
Illustration - Adonay Gebru
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs