Mphatso ya agogo akazi
Sibongile Mnkandla
Sibongile Mnkandla

Agogo akazi akubwera kudzatiyendera. Nthawi zonse amamubweretsera Thabo mtedza ndi zipatso za mtchire, kapena chimanga chachiwisi ndi chivwende.

Thabo akufuna kuwapatsa Agogo chinthu cha mtengo wapatali.

1

Buku litha kukhala mphatso yabwino kwambiri, koma kodi Agogo amatha kuwerenga?

Kodi atapita kukagula kumasitolo, atha kukapeza chinthu chosangalatsa?

"Tiyeni tiwapangire chikwama," anatero Thabo mwachimwemwe. "Chikwama chachikulu cholimba cha mtundu wa buluu."

2

Amayi atenga nsalu imene anagula kusitolo. Atambasula muyeso ndi kuyamba kudula.

Ayamba ndi mbali ziwiri zimene ndi zotambalala komanso zazikulu.

3

Kenako mbali zing'onozing'ono ziwiri kuti chikhale ndi maonekedwe abwino.

Thabo azipinda limodzi ndi mbali zikuluzikulu ziwiri zija. Akuwonerera pamene Amayi akuyesa kachikena.

4

Adula zidutswa ziwiri m'munsi mulitali. Izi ndi zimene zichititse chikwama kukhala cholimba.

Thabo akupinda pamene Amayi akuyesanso.

5

Adula zidutswa zinayi zomwe ndi zotambalala komanso zazitali.

Ziwiri zisokedwa limodzi kupanga lamba m'modzi. Izi zilimbitsa chikwama kwambiri.

6

Kenako Amayi atenga makina awo osokera.

Alumikiza zidutswa zonse kupanga chikwama cha Agogo akazi.

Achipereka kwa Thabo amene amwetulira ndi kunena kuti, "Zikomo Amayi posoka chikwama cha Agogo akazi."

7
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mphatso ya agogo akazi
Author - Sibongile Mnkandla
Translation - Peter Msaka
Illustration - Sibongile Mnkandla
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs