

Nita walendewera chozondoka, tsitsi lake likugunda pansi.
Mitengo, udzu ndi zina zonse zaima molakwika.
Miyendo yake, ikuloza kumwamba. Kamnyamata kakang'ono dzina lake Navi kakudutsa.
"Iwe ndakupezanso pano. Chifukwa chiyani wakhalanso chozondoka?"
Miyendo ya Navin ikuyenda mmalelere. Nita ayesera kubisala kuseli kwa tsitsi lake.
"Ndi-ndi-ndi-ndizovuta ku-ku-ku-yankhula," atero Nita kwa Navi. "Sindilinso chimodzimodzi. Sindilinso ngati aliyense."
Navi amugwira Nita pa mkono. Akufuna kumuthandiza kuti amvetse. Akwera mumtengo, malo amene Navi amakonda kukwera akafuna kuona patali.
Kuchokera mumtengomo akutha kuona kutali. Akhala pa nthambi ndikumaona ana akusewera mmalo osiyanasiyana.
Ana aja salinso chimodzimodzi. Abe wanenepa kwambiri.
Nkhope ya Chi ili ndi ziphuphu.
Lala watalika.
Bambam ndi ovuta ndipo safuna kuletsedwa.
Pamene Lulu akuwerenga mwachinunu.
Taonani tsitsi losapesa la Freya.
Ndipo Sidi akuvala magalasi kuli konse.
Pamene ine, ndine khungu ndi mafupa okhaokha. Koma iwe ndi iweyo. Suli wekha. Munthu aliyense ndi osiyana ndi mzake.
Izi zichititsa iwe kufanana ndi ine. Dziko lonse lili ngati masewera akulu zedi. Kuti tisewere, tiyenera kukhala osiyanasiyana.
Nita ayamba kumva bwino, amuthokonza mzake watsopanoyu.
Kukhala chozondoka sizinali zinthu zabwino. Tsopano akusewera ndi wina aliyense.


