Tamara ayamba sukulu
Soila Murianka
Jacob Kono

Tamara anali mtsikana wa zaka zisanu amene amakhala ndi banja la kwawo.

Mudzi wawo unali pafupi ndi nkhalango yomwe munali nyama za kutchire.

1

Tamara anali mwana womvera makolo ake.

Amadyetsa nkhosa ndi mbuzi.

2

Tamara amakonda kumvetsera kuyimba kwa mbalame pamene amadyetsa ziwetozo.

Pamene mbalame zimayimba, Tamara amayika mawu ake m'mingoli ya mbalamezo.

3

Tamara sanali wa msinkhu wopita ku sukulu. Makolo ake analola Nashipae ndi Tasieku kupita ku sukulu.

Sukuluyi inali pa mtunda wa makilomita khumi.

4

Nashipae ndi Tasieku amapita ndi ana anzawo a m'mudzi. Amapita m'mawa ndipo amabwerako madzulo.

Amanyamula zakudya zawo m'makontena.

5

Tamara anafunsa amayi ake, "Kusukulu ndidzapita liti?

Amayi ake anayankha, "Upita posachedwa apa, mwana wanga."

6

Tsiku lina, kunafika amfumu ndi amayi awiri pa galimoto.

Amfumuwa amaonetsetsa kuti ana akupita ku sukulu pa msinkhu wabwino.

7

Anthu amakhulupirira kuti ngati mwana watambalitsa dzanja lake pa mutu ndi kugwira khutu, anali woyenera kuyamba sukulu.

8

Amfumu anafunsa, "Uli ndi zaka zingati?" Tamara anayankha, "Ndili ndi zaka zisanu."

"Tiyeni tiwone ngati ungayambe kupita ku sukulu," amfumu anatero.

9

Mzimayi m'modzi anagwira dzanja la Tamara la ku manja ndi kulitambalitsa pa mutu wake.

Tamara anagwira khutu la ku manzere.

10

Tamara azipita ku sukulu yosiyana ndi ya Nashipae ndi Tasieku.

Inali sukulu yatsopano ndiponso ya pafupi ndi nyumba yawo.

11

Tamara anasangalala kwambiri.

"Ndiziwerenga ndi kulemba ngati Nashipae ndi Tasieku." Anaganiza motero.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Tamara ayamba sukulu
Author - Soila Murianka
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Jacob Kono
Language - Chichewa
Level - First paragraphs