Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo
Khothatso Ranoosi
Children of Paleng

Kalekale, Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo zimamenyana.

1

Vuto linali lakuti, Dzuwa limafuna kuwala tsiku lonse. Mwezi umafuna kuwala tsiku lililonse.

Mvula imafuna kugwa tsiku lililonse ndipo Mphepo imafunanso kuomba tsiku lililonse. Samafuna kupatsana mpata.

2

Anaganiza zokhala pamodzi ndi kukambirana.

Dzuwa linafunsa Mwezi, "Kodi umachita chiyani chimene chimathandiza dziko?"

Mwezi unayankha, "Ndimawala usiku kuti nyama zizisaka."

3

Mwezi unafunsa Mvula, "Kodi umachita chiyani chimene chimathandiza dziko?"

Mvula inayankha, "Ndimapereka madzi ku dziko kuti mitengo ndi zomera zizikula. Ndimaperekanso madzi kwa nyama kuti zizimwa."

4

Mvula inafunsa Mphepo, "Kodi umachita chiyani chimene chimathandiza dziko?"

Mphepo inayankha, "Ndimasesa dziko kuti lizikhala loyera. Ndimagawanso mvula ku dziko lonse."

5

Mphepo inafunsa Dzuwa, "Kodi umachita chiyani chimene chimathandiza dziko?"

Dzuwa linayankha, "Ndimapereka kuwala ndi kutentha kudziko, kuti nyama ndi zomera zikhale moyo."

6

Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo anamvetsetsana zomwe aliyense ananena.

7

Dzuwa linati, "Nzoona kuti aliyense pano amathandiza dziko munjira zosiyanasiyana." Mwezi unavomereza, "Zoona. Palibe pagulu lathu lino amene ndi ofunika kuposa mzake."

"Titha kugwirira ntchito limodzi," Mvula inanena. Kenako Mphepo inati, "Ndiye tiyeni tigawane masiku." Onse anagwirizana.

8

Ndi chifukwa chake nthawi zina mumaona mwezi ukuwala pamene dzuwa likuwalaso. Nthawi zina mumaona kuomba kwa mphepo pamene mvula ikugwa.

Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo zimagwirira ntchito limodzi. Zimamvetsana.

9

Kodi umakonda dzuwa, mwezi, mvula kapena mphepo? Jambula chimene umakonda.

10

Timadalira dziko kuti tikhale moyo. Dziko limatipatsa chakudya, pogona, nyama ndi zomera. Zonse zimatithandiza ife munjira zosiyanasiyana. Ndipo titha kubwezera zabwinozi kuti tithandize dziko lathu. Kodi udzatani kuti uthandize dzikoli? Lemba zomwe udzachite.

11
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo
Author - Khothatso Ranoosi
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Children of Paleng
Language - Chichewa
Level - Longer paragraphs