Mafunso a Kariza
Jean de Dieu Bavugempore
Rob Owen

Kariza amakonda kufunsa mafunso. Anatengera khalidwe limeneli kwa makolo ake.

Makolo ake amakonda kumuuza kuti, "Ngati sufunsa mafunso uli wamng'ono, udzakula munthu osadziwa zinthu."

1

Tsiku lina, Kariza anafunsa aphunzitsi ake, "Ndi chifukwa chiyani makolo athu amatiuza kuti tizisamba m'manja tisanayambe kudya, ngakhale kuti m'manja mwathu ndi moyera?"

Ophunzira anzake analikonda funso la Kariza. Sizimawasangalatsa zouzidwa kuti azisamba m'manja.

2

Aphunzitsi anayankha, "Funso labwino! Ngakhale manja athu amaoneka oyera, atha kukhalabe ndi majeremusi."

Anafotokoza motere, "Majeremusi amayambitsa matenda. Sitingawaone majeremusi ndi maso athu, timayenera kugwiritsa ntchito chipangizo champhamvu kwambiri kuti tiwaone."

3

Aphunzitsi anatulutsa maikolosikopu kuchokera mu kabati. Aphunzitsi anafotokoza motere, "Maikolosikopu ndi makina amene timagwiritsa ntchito kuona tizilombo ting'onoting'ono timene maso paokha sangaone."

Aphunzitsi anapala m'manja mwa Kariza ndi kamtengo kenako anaika topalidwato pa galasi loika pa maikolosikopu.

4

Kenako aphunzitsi anaika galasilo pa maikolosikopu ndipo izi ndi zimene anaona.

Ngakhale m'manja mwa Kariza mumaoneka moyera, m'manjamo munali majeremusi.

5

"Paliponse pali majeremusi, pa zinthu zimene timagwira m'kalasi mwathu, kubwalo la masewera kapena kunyumba.

Majeremusi amenewa atha kutidwalitsa kwambiri," anachenjeza aphunzitsi.

6

Aphunzitsi anapitiliza kufotokoza, "Kuti tiwaphe majeremusi amenewa, tiyenera kusamba m'manja ndi madzi oyera ndi sopo, makamaka tisanayambe kudya.

Komanso, tikadwala tiyenera kusamba m'manja kuti tisafalitse majeremusi."

7

Atabwerera kunyumba, Kariza anapeza bambo ake akupanga chinthu chopatsa chidwi. "Mukupanga chiyani?" Iye anafunsa.

"Ichi chimatchedwa 'pondausambe,'" bambo ake ananena. "Timagwiritsa ntchito posamba m'manja."

8

Kariza anadabwa ndipo anati, "Oh zoona! Aphunzitsi athu anatiuza za chipangizo chimenechi. Koma ambiri sitimachidziwa. Chimagwira ntchito motani?"

Abambowo anaseka ndi kumuuza kuti, "Bwera pafupi ndikuonetse mwana wanga."

9

"Choyamba, ponda pa thabwa lili pansili," anatero bambo ake.

10

"Ukatero, chigubu cha madzi chidzapendekera ndipo madzi adzathikira m'manja mwako.

Kumbukira kusamba ndi sopo," anamuuza Kariza.

11

Kariza anasangalala ndipo anati, "Ndikanadziwa bwanji izi popanda kufunsa mafunso?

Ndi zoona kuti kufunsa kumabweretsa kudziwa."

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mafunso a Kariza
Author - Jean de Dieu Bavugempore
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Rob Owen
Language - Chichewa
Level - Longer paragraphs