

Uyu ndi Mphaka.
Uyu ndi Galu.
Mphaka ndi Galu akufuna kujambula.
Mphaka ndi Galu akufuna kupenta.
Mphaka ndi Galu akufuna kupanga za luso.
Galu ayamba.
Watenga pensulo ndi pepala. Pepalali ndi la sikweya.
Poyamba Galu ajambula chithunzi chozungulira ngati dzira.
Chithunzi chozungulirachi ndi thupi la Mphaka.
Aaaa, ndizophweka!
Kenako, ajambula mathilayango awiri pamwamba pa chozunguliracho.
Mathirayango awiriwa ndi makutu a Mphaka ndipo ajambula thirayango ya kuda mkati mwa chithunzi chozungulira chija.
Thirayango ya kudayi ndi mphuno ya Mphaka ndipo ajambula mzere pamwamba pa mphuno.
Tsopano ajambula maso ndi nsidze za Mphaka.
Masowa ndi madontho awiri.
Nsidze ndi mizere iwiri.
Aaa, ndi zophweka.
Kenako, ajambula kamwa la Mphaka.
Kamwalo ndi mzere umodzi.
Ukuwoneka ngati chilembo cha 'W', ndipo kenako ajambula ubweya wa Mphaka.
Ubweya utatu mbali ya kumanzere, ndipo utatu kamanja.
Chithunzichi chatsala pang'ono kumalizidwa.
Kenako, ajambula manja ndi miyendo ya Mphaka.
Manja ndi miyendo ndi mizere, kenako ajambula zala za Mphaka.
Zalazi ndi kanthu kozungulira, kenako ajambula mchira wa Mphaka.
Mchira ndi mzere wawutali.
Pomaliza ajambula mizere yoyera ndi yakuda pa thupi la mphaka. Ndipo apaka utoto wa orenji.
Chithunzi chamalizidwa.
Ooo! Chikuoneka bwino kwambiri.
Tsopano ndi nthawi ya Mphaka.
Iye atenga pensulo ndi pepala.
Pepala ndi la lekitango.
Poyamba Mphaka ajambula chithunzi chozungulira ngati dzira.
Chithunzi chozungulirachi ndi thupi la Galu.
Oooo! Zili bwino!
Kenako ajambula tinthu tiwiri takuda pamwamba pa thupi la galu.
Tinthu tiwiri takuda ndi makutu a Galu, kenako ajambula kanthu kakuda kozungulira mkati mwa thupi la Galu.
Kanthu kakuda kozungulira ndi mphuno ya Galu, kenako ajambula mzere pamwamba pa mphuno.
Tsopano ajambula maso ndi nsidze za galu.
Nsidze ndi mizere iwiri.
Ooo! Zili bwino!
Kenako ajambula kamwa la Galu.
Kamwa ndi mzere umodzi.
Kaonekedwe kake kali ngati chilembo cha 'W', ndipo ajambula madontho kuzungulira kamwa la Galu.
Atatu kumanzere ndi atatu ena kumanja.
Chithunzi chatsala pang'ono kumalizidwa.
Ajambula manja ndi miyendo ya Galu.
Manja ndi miyendo ndi mizere, kenako ajambula zala za Galu.
Zala ndi tinthu tozungulira, kenako ajambula mchira wa Galu.
Mchira ukuoneka ngati duwa.
Pomaliza, ajambula tinthu tozungulira takuda pa thupi la Galu ndipo apaka utoto wa chikasu pathupi.
Chithunzi chatha kujambulidwa.
Oooo, chikuoneka bwino.
Ndapita Mphaka.
Ndapita chithunzi cha Mphaka.
Ndapita Galu.
Ndapita chithunzi cha Galu.

