

Kunali mnyamata wina, dzina lake Abel. Anadzipangira ngolo yoti aziseweretsa.
Abel analibe woyendetsa ngolo yakeyo. Anamuuza mchemwali wake Meri, "Ndikufuna oyendetsa ngolo yanga. Chonde ndipatse chidole chako. Chitha kukhala m'ngolomu."
Koma Meri anati, "Ayi, ndikufuna chidole changa." Meri atakaniza chidolecho, Abel anakwiya kwambiri.
Anagwira chidolecho ndi kuyamba kuchikoka. Meri anakoka dzanja lina la chidolecho. Abel anakoka ndipo Meri anakokanso. Kenako dzanja la chidolecho linazukamo.
Meri analira ndi kuthamangira kwa amayi ake. Meri anati, "Onani amayi. Abel anakoka dzanja la chidole ndipo lazuka. Amafuna chidole changa kuti chikhale mngolo yake koma ndimafuna ndizisewera nacho."
Mayi ake anayankha, "Abel sanachite zabwino."
Amayi anaganizira za njira yomuphunzitsira Abel kuti asamagwire zidole za mchemwali wake. Anapeza ganizo labwino.
Anapita kwa mzawo amene anali dokotala. Atafika anafunsa, "Ndikufuna mundithandize." Adokotala aja anayankha, "Ndikuthandize bwanji mzanga?"
Amayi aja anati, "Mwana wanga Abel akuonetsa khalidwe loipa masiku ano. Wazula dzanja la chidole cha mchemwali wake. Sakuyenera kuchita zimenezi.
Mawa ndimutuma kuti abweretse chidolecho kwa inu kuti mudzaikireko dzanja lina."
"Mumuuze Abel kuti akulipireni pa ntchito imeneyi. Alibe ndalama, ndiye mudzamuuze kuti atsuke galimoto yanu yaikulu imene imakhala ndi fumbi nthawi zonse ija," anatero mayiwo.
Mzawoyo anaseka ndikunena kuti, "Ee-ee! Zimenezi zidzakhala zabwino."
Amayi aja anabwerera kunyumba. Anamufunsa Abel, "Kodi ukadwala kapena kuvulala, umapita kuti?" Abel anayankha, "Ndikadwala kapena kuvulala ndimapita kwa adokotala."
Amayi a Abel anati, "Wavulaza chidole, tsopano uyenera kuchitengera kwa adokotala."
Kotero, Abel anachitengera chidole chija kwa adokotola. "Chidole ichi chavulala kwambiri. Amayi anga andiuza kuti ndichibweretse kwa inu. Adokotala, mungachiikire dzanja lina?"
Adokotala anavomera. Ndipo anakwanitsa kuchipangira dzanja lina.
Adokotala anamuuza Abel, "Chidole chili ndi dzanja lina tsopano. Uyenera kundilipira. Uli ndi ndalama zingati?"
Abel anayankha, "Chonde adokotala, ndilibe ndalama. Sindingathe kukulipirani pa ntchito mwagwirayi."
Adokotala anati, "Chabwino, ulibe ndalama eti? Galimoto yanga yaikulu ija ndiyakuda kwambiri. Uitsuke galimotoyi ndipo ndi mmene undilipilire."
Abel anatenga ndowa ya madzi ndi nsalu yoyera. Zinamutengera nthawi yaitali kuti amalize kutsuka galimotoyo.
Kenako Abel anakachibweza chidole chija kwa Meri. Meri anakondwa kwambiri ndipo anamuuza Abel kuti, "Ndiwe mchimwene wabwino. Zikomo kwambiri pokonza chidole changa."
"Mchemwali wanga, ndikukupepesa chifukwa ndinakwiya ndi kukukhumudwitsa," Abel anapepesa motero.
Kuchokera tsiku limenero, Abel sanatengenso zinthu za mchemwali wakeyo. Ndipo anayesetsa kupewa kumukwiira mchemwali wakeyo.
Abel anakumbukira nthawi yayitali yomwe anatenga kuti amalize kutsuka chigalimoto cha adokotala chija. Ndipo anaganiza kuti zinalibe phindu kukwiya ndi kuphwanya zinthu.

