Manja anga okongola
Mokoena. M. Alphonsina
Mokoena. M. Alphonsina

Awa ndi manja anga okongola. Amagwira bwino nchito pamodzi.
Alingati abwenzi awiri abwino. Amapanga gulu labwino kwambiri.

1

Monga abwenzi abwino osatayana, pamene lina lakhala ndi dothi, linali lilipo kuti lisambike linzake.
Ali okonzekera kuthanzirana.

2

Amagwira nchito pamodzi ngati gulu.

3

Pamene chakudya chiphikidwa, manja onse awiri amagwira nchito yabwino pamodzi ngati gulu.

4

Dzanja la manja lilipo nthawi zonse kuthandizira dzanja lamanzere.

5

Dzanja lamanzere lilipo nthawi zonse kuthandizira dzanja la manja.

6

Monga abwenzi awiri othandizirana, okondeka ndi osamalirana, manja anga okongola amayang'anirana.

7
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Manja anga okongola
Author - Mokoena. M. Alphonsina
Translation - Agnes Nankhoma-Singine Nyendwa
Illustration - Mokoena. M. Alphonsina
Language - Chichewa
Level - First sentences