Nyani ndi Ng'ona
Mulualem Daba
Abraham Muzee

Nyani akumana ndi Ng'ona ku nyanja,

1

"Kodi ukhala kuti?" Nyani anafunsa, "Mnyanja, "Ng'ona inati.

2

"Ukhala kuti?" Ng'ona inafunsa. "Mumitengo, "ananena Nyani.

3

"Kodi ungathe kusambira?" inafunsa Ng'ona.

4

"Sinditha kusambira" Nyani anati. "Ndingathe kukuphunzitsa."

5

"Ndife abwenzi. Osaopa," inanena Ng'ona.

6

"Nyani, amalume anga ndiwodwala. Afunikira nyama," Ng'ona inati.

7

Nyani anaopa kwambiri. Kodi Ng'ona ingamudye?

8

Nyani afuna kuthawa Ng'ona.

9

Nyani ali ndi nzeru ina.

10

"Ndidzawapatsa mtima wanga," Nyani analonjeza.

11

"Mtima wanga uli mumtengo kumtunda, Nyani anati.

12

"Kodi udzapita kukatenga mtima wako?" Inafunsa Ng'ona. "Inde," Nyani anati.

13

Ng'ona inabwerera kumtunda. Nyani anathawira m'mitengo.

14

"Sindiwe bwenzi langa. Wanama bodza! Ng'ona inanena.

15

"Sindife abwenzi. Ufuna kundidya!" ananena Nyani.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nyani ndi Ng'ona
Author - Mulualem Daba
Translation - Agnes NankhomaSingine Nyendwa
Illustration - Abraham Muzee
Language - Chichewa
Level - First words