

Luwo anapita ku tchalitchi ndi mayi ake.
Iye anali atagwidwa dzanja mu njira.
Mkati mwa tchalitchi munali anthu ambiri omwe anasonkhana.
Iwo anali kuyimba.
Luwo anachoka m'tchalitchi.
Ndipo mayi ake sadamuone iye.
Luwo anaima panjira.
Iye anayang'ana pansi nadzifunsa kuti, "Kodi nyumba yathu ili kuti?"
Kotero iye ankatsatira njira.
Iye adaona nyumba yaikulu, ndipo iye anati, "Ayi, sinyumba yathu, nyumba yathu ndi yaing'ono."
Luwo anayenda pang'ono. Iye anaona nyumba pa nsanja.
Iye anati, "Ayi, iyo sinyumba yathu. Nyumba yathu siili pa nsanja."
Iye adapitiliza kuyenda. Iye anaona nyumba ya udzu.
Ndipo iye anati, "Ayi, iyo sinyumba yathu. Nyumba yathu ili ndi makoma amatope."
Luwo anapita patsogolo. Anaona nyumba yaing'ono ndi mtengo wa mango kunja.
Ndipo iye anati, "Ayi, sinyumba yathu. Nyumba yathu ili ndi mitengo iwiri ya mango panja."
Pamapeto pake Luwo anaona mayi ake akubwera kwa iye. Luwo anathamangira kwa mayi ake.
Ndipo mayi ake anati, "Tiye kunyumba kwathu!"
Kodi nyumba ya Luwo ndi iti?

