Ng'wena Muthupi Mwanga
Val Morris
Felicity Bell

Moni, moni, zina langa ndine Ntombi. Ndine msikana monga asikana ena onse, koma nisiyana na ena cifukwa nili na ng'wena mu thupi mwanga. Imwe simungayione ng'wena iyi koma ine niziwa kuti iliko. Zina la ng'wena ni Horrible InVader. Ng'wena iyi ibisala mumubili wanga ndipo siyingacite coipa ciliconse kuli anzanga.

1

Iyi ng'wena siyingacoke mu tupi mwanga nakulowa mutupi mwako ngati wakala pafupi na ine.

2

Iyi ng'wena siyingacoke mu tupi mwanga nolumpila mutupi mwako tikadya cakudya pamozi, mwina tikagona pansi pamozi kuti tipumule.

3

Ng'wena yanga, Horrible InVader, akala mutupi mwanga kucokela pamene ninabadwa. Horrible InVader akonda kudya asilikali onse amutupi mwanga amene amenya nkondo na zilombo zomwe zinganidwalise.

4

Nimafunika kumwa mankwala anga masiku onse pa ntawi yake. Ngati sinikwanilisa kumwa mankwala, ng'wena imauka ndipo imakala yokwiya kwambili ndipo imayamba kudya asilikali anga. Sinifuna kuti ng'wena idye asilikali anga, nicifukwa cake nimakumbusa aGogo anga kuti anipase makwala anga pantawi yake.

5

Ngati nikudya cakudya cofunikila monga vipaso nandiwo za masamba, asilikali anga azakala nampamvu ndipo sangaleke kuti ng'wena iwagwile. Niganiza kuti ng'wena imagona kwanthawi itali cifukwa tupi yanga ili na mpamvu ndipo nikwanisa kusowela na anzanga. Ndimakondwela kwambili ngati ng'wena yagona ndipo nikwanisa kusowela.

6

Masiku apitapo, aGogo ananipeleka ku cipatala kukatenga zina zodyesa ng'wena. Izi zigonesa ng'wena, ndipo ileka kudya asilikali anga. Ndipo nimakwanisa kucita zonse zosangalasa zamene acita ana ena monga, kutamanga, kuvina ndi kukwela mtengo.

7

Niwakonda kwambili aGogo anga. Anisamalila ndipo anisunga bwino. Amanipasa cakudya ndipo amanipasa mavitamini ena kuti nimwe kuti asilikali anga akale nampamvu, kuti nisazidwala. Ngati nadwala amanipeleka mwamsanga-msanga kucipatala kuti nikatenge mankwala onicilisa. Nimakondwela ngati nakala pamendo pa aGogo ndipo aniwelengela ntano nikalibe kugona.

8

Akanipeleka kugona aGogo, nimaganizila zintu zambili. Nimaganizila kupunzila kuwelenga kusukulu yaikulu. Ngati napitiliza kumwa mankwala anga amene agonesa ng'wena, nizayamba kuwawelengela ntano aGogo akakalamba kwambili ndipo aleka kuona bwino. Nikakula ningafune kupunzila. Nifuna kutandiza kupeza mankwala amene azagonesa ng'wena zonse zomwe zikala munatupi a antu kuti zikagoneletu.

9

Nizapunzila kukala na ng'wena yanga ndi kuyisunga yogona monga mwamene ningakwanilisile. Nizakala na anzanga ambili monga mwamene ningakwanilisile. Nizasobela kwambili monga mwamene ningakwanilisile.

10

AGogo, amalume, amai aang'ono, anzanga anikonda ngakale kuti nili na ng'wena yocedwa Horrible InVader yamene ikala mutupi yanga.

11
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Ng'wena Muthupi Mwanga
Author - Val Morris
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Felicity Bell
Language - CiNyanja
Level - Read aloud