

Nita ali ogadama. Sisi lake lalitali lifika pansi. Mitengo, mauzu ndi zonse zili zogadama.
Mapazi a Nita ali mumwamba. Navi apita. "Nimakuona pano nicifukwa ninji ukonda kunkala cogadama?" Navi afunsa.
Nita asobelesa mapazi mumpepo. Ayesesa kubisamila musisi yake. "Nicosapepuka kukamba," Nita auza Navi. "Ndine osiyana ndi ana ena. Nilepela kusowela nao."
Navi afuna kutandiza Nita. Atenga Nita nakwela naye mutengo. Pamwamba pa mutengo baona zambili. Bose babili bapenyelela ana amene asowela pansi.
Ana awa niwosiyana siyana. Abe niwathupi.
Chi ali ndi tumabamba kumenso.
Lala niwamutali kwambili.
Bambam niwomasuka.
Lulu abelenga mumtendele.
Ona sisi yosokonezeka ya Freya.
Sid avala ma gilasi kulikonse.
Ine ndine oyonda kwambili. Iwe ndi iwe. Suli paweka ayi. Muntu ali yense nowosiyana ndi ena. Kuti tisewele, tiyenela kunkala osiyanasiyana.
Nita amvela bwino sopano cifukwa ca munzake wamene apeza. Kunkala chogadama sicabwino. Nita asowela ndi anzake.


