

M'bale wanga amacedwa kuuka.
Ine nimauka kuseni seni cifukwa ndine opambana.
Nimasegula mazenera kuti zuwa lingene.
"Ndiwe ntanda yanga," anena amai.
Nimazisambika masiku onse kopanda tandizo lililonse.
Sinivutika kusamba manzi ozizila kapena kusambila sopo yobiliwila yocapila zovala.
"Osaiwala kusuka mano," akumbusa amai.
Niyanka kuti, "Sicingacitike kuli ine."
Pambuyo posamba, nipeleka moni kwa ambuya na amayi aang'ono.
Ndipo nimazivalika zovala.
Nimanena kuti, "Ndine wamukulu sopano amai."
Nimakwanisa kumanga ma batani ndiponso kumanga nthambo za nsapato zanga.
Nimasimikiza kuti m'bale wanga aziwa nkhani zonse zakusukulu.
Kusukulu nimayikako nzelu mu zonse.
Nimacita zonse izi zabwino masiku onse.
Koma camene nikondesesa kwambili nikusowela, kuswowela ndi kusowela!

