Nema agula Ulusi
Little Zebra Books
Mirjam Gyger

Uyu ni Nema.

Nema akusoka.

Nema akusoka ndiloko.

1

Nema, asoka na ulusi. Ulusi wasila. Nema akufuna kukagula wina ulusi.

Akufuna ndalama zokagulila. Kodi iye azipeza kuti ndalama?

2

Nema aona mtengo. Mtengo uli pafupi.

Mumtengo muli zipaso. Zipaso zake ni mapapaya. Papaya ndilotsekemela.

3

Nema ali ndi ntokoso.

Nema agwesa mapapaya.

4

Nema afika kumsika.

Iye afika kumsika na mapapaya.

Iye afuna kugulisa mapapaya.

5

Onani abambo. Abambo agula papaya limodzi.

Iwo apeleka ndalama kwa Nema. Nema agulisa mapapaya ambili.

Nema alandila ndalama yomwe azagulila ulusi.

6

Kumsika, aona ntoci.

Iye sagula ntoci.

7

Kumsika aona matimati.

Iye sagula matimati.

8

Kumsika aona sefa.

Iye sagula sefa.

9

Kumsika aona buledi.

Iye sagula buledi.

10

Nema aona abambo.

Abambo akugulisa ulusi.

Nema agula ulusi.

11

Nema ali ndi ulusi.

Nema ali osangalala.

Iye amaliza kusoka ndiloko ndi ulusi.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nema agula Ulusi
Author - Little Zebra Books
Translation - Little Zebra Books
Illustration - Mirjam Gyger
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs