

Sara ali na ngalawa imodzi.
Ngalawa yake ni yaikulu.
Ngalawa ili mumpepete mwa musinje.
Azimai ali pamusinje. Mai umozi ali ndi beseni. Mubeseni muli zipaso. Mai wina watenga mbuzi imozi. Mai winanso watenga mbuzi ziwili.
Iwo afunsa Sara: "Tingafike bwanji sidya ilo?"
Sara anena: "Lowani mungalawa yanga!"
Posatila, afika azibambo. Bambo umozi watenga nsomba. Wina ali ndi njinga. Winanso watenga katumba momwe muli mteza.
Bambo wina watenga tumatumba tuwili momwe muli mteza.
Iwo afunsa Sara: "Tingafike bwanji sidya ilo?"
Sara anena: "Lowani mungalawa yanga!"
Nyama zina, zafika ku msinje.
Izo zifunsa Sara: "Tingafike bwanji sidya ilo?"
Sara anena: "Lowani mungalawa yanga!"
Nyama zilowa mungalawa.
Galu alowa mungalawa.
Cona alowa mungalawa.
Nyani alowa mungalawa.
Kalulu alowa mungalawa.
Kamba alowa mungalawa.
Gwape alowa mungalawa.
Njobvu ifika pamusinje. Iyo ifunsa: "Ningacite bwanji kuti nifike sidya ilo?"
Sara anena: "Lowani mungalawa yanga!"
Njobvu ilowa mungalawa. Manzi azula mungalawa.
Ngalawa niyingono kwambili. Malo niyocepa.
Sara anena: "Iiiiiii! Yembekezani ntawi pangono. Coyamba nizanyamula azimai."
"Kaciwili, nizatenga azibambo."
"Pomaliza nizatenga nyama."
Njovu inena: "Iiiiiii! Ine niwoloka pansi!"

