Cona na Galu ajambule na kupenta
Elke and René Leisink
Elke and René Leisink

Uyu ni Cona.

Uyu ni Galu.

1

Cona na Galu afuna kujambula.

Cona ndi Galu afuna ku penta.

Chona ndi Galu afuna kupanga zintu za luso.

Galu ayamba.

Galu atenga pensulo na pepala lofanana mbali zones muutali.

2

Paciyambi Galu ajambula cifanizo ca ovo.

Fanizo ni tupi la Cona.

Ahede, ico ni copepuka!

3

Ndipo ajambula ma tilayango awili.

Ma tiliyango awili ni matu ya Cona. Ndipo anajambulanso tilayango yakuda, mukati mwa ovo.

Tiliyango yakuda ni mpuno ya Cona. Ndipo anajambula kamuzele pa mwaba pa mpuno.

4

Sopano ajambula maso na nsize za Cona.

Maso ni madonto awili.

Nsize ni mizela ziwii.

Ahede, ni copepuka!

5

Ndipo anajambula kamwa ka Cona.

Kamuzela ndiko kamwa.

Kaoneka monga lembo la 'W' ndipo anajambula ubweya wa Cona.

Ubweya utatu ku zanja la manzele ndiponso ubweya utatu ku zanja lamanja.

6

Chitunzi chili kumapeto.

Anajambula manja na mendo ya Cona.

Ndipo anajambulanso zala zakumyendo ya Cona.

Ndipo amajambulanso muchila wa Cona.

Muchila ni ka muzele katali.

7

Pomaliza anajambula tumizele pa tupi la Cona na kupenta mutundu waolenji.

Chitunzi chata.

8

Sono ni ntawi ya Cona.

Atenga pensulo na pepala ya lekitango.

9

Coyamba Cona anajambula ovo.

Ovo ni tupi la Galu.

Ahede, ico ni cabwino!

10

Anajambula kofanana na matepo awili akuda pamwamba pa ovo.

Tofanana na matepo awili akuda ni matu a Galu.

Ndipo anajambula ovo ya kuda mukati mwa ovo.

11

Sopano ajambula maso na nsize za galu.

Maso yanali madonto awili. Nsize zinali mizela ziwili.

Ahede, manje zakoma!

12

Sopano ajambula kamwa ka Galu.

Kamwa ni muzele.

Ndiponiso kaoneka ngati lembo la "W". Sopano ajambula madonto ku zunguluka kamwa ka Galu.

Yatatu ku zanja la manzele ndiponso yatatu ku zanja la manja.

13

Citunzi cili ku mapeto.

Ajambula manja na myendo ya Galu.

Manja na myendo ni mizele ndipo ajambula zala zaku myendo za Galu.

Zala ni maseko. Sopano ajambula muchila wa Galu. Muchila uoneka monga luba.

14

Kumapeto, ajambula ma seko okuda pa tupi la Galu ndiponso apenta tupi na cikasu.

Citunzi cata.

Ahede, zakoma!

15

Tionane Cona.

Tionane citunzi ca Cona.

Tionane Galu.

Tionane citunzi ca Galu.

16

17
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Cona na Galu ajambule na kupenta
Author - Elke and René Leisink
Translation - Lusaka Teachers
Illustration - Elke and René Leisink
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs