

Kalulu anali gone munsi mwa mutengo. Cipaso cinagwa pansi kucokela mu mutengo.
Anamvela mau akuti, "Taba Kalulu taba!" Kalulu anauka mwamusanga-musanga nataba luwilo lalukulu.
Kalulu anakumana na Nkuku. "Utaba cani?" inafunsa Nkuku. "Siniziba, namvela cabe cintu cagwa, na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Nkuku inayopa. Inayamba kutaba pamene inamvela mau a Kalulu.
Nyama izi zinanakumana na Imbwa. Imbwa inafunsa, "Mutaba cani?" Nkuku inati, "Siniziba, namvela cabe vamene akamba Kalulu koma naye saziba. Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Imbwa inadabwa navamene inamvela. Ndipo inayamba kutaba na kalulu na Nkuku.
Nyama izi zinakumana na Hosi. Hosi inafunsa, "Mutaba cani?" Imbwa inati, "Siniziba, namvela cabe vamene akamba Nkuku koma naye siyiziba. Nkuku amvela vamene akamba Kalulu kuti Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Hosi nayo inayamba Kutaba.
Nyama izi zinakumana na Bulu. Bulu anafunsa, "Mutaba cani?" Hosi inati, "Siniziba, namvela cabe vamene yakamba Imbwa, koma nayo siyiziba. Imbwa yamvela vamene akamba Nkuku, koma naye saziba. Nkuka amvela vamene akamba Kalulu kuti Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Bulu nayo inayamba kutaba.
Zinakumana na Ng'ombe. Inafunsa, "Mutaba cani?" Bulu inati, "Siniziba, namvela cabe vamene akamba Hosi, koma naye saziba, amvela vamene yakamba Imbwa, koma nayo siyiziba. Imbwa yamvela vamene akamba Nkuku, koma nayo siyiziba. Nkuka amvela vamene akamba Kalulu kuti Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Ng'ombe inayopa noyamba kutaba nayo.
Kiti inafunsa, "Mutaba cani?" Ng'ombe inati, "Siniziba, namvela cabe vamene akamba Bulu, Bulu naye saziba, amvela vamene yakamba Hosi, koma nayo siyiziba. Hosi yamvela vamene yakamba Imbwa, koma nayo siyiziba. Yamvela vamene akamba Nkuku, koma nayo siyiziba. Nkuku amvela vamene akamba Kalulu kuti Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Kiti naye anayamba kutaba navinyama vonse.
Ndipo vinyama vinakumana na munyamata acova njinga. Munyamata anafunsa, "Mutaba cani?" Vinyama vinati, "Sitiziba. Tamvela vamene akamba Kalulu, koma naye saziba. Kalulu amvela cintu cagwa na mau akuti 'Taba Kalulu taba!'"
Munyamata anaseka nati, "Cipaso cinali cagwa kucokera mu mtengo cifukwa ca cimpepo. Ine ndine nauza Kalulu kuti, 'Taba Kalulu taba!'"

