Osunga nyama pamalo posungila nyama zing'ono
Ursula Nafula
Magriet Brink

Iyi ni nkani ya tumyama twamasiye.

1

Mwezi wasila, antu osunga tunyama twamasiye, anali na ncito kwambili. Kanyama ka caka cimozi ndiye kanayambilila kufika pamalo apa.

Zina lakanyama aka linali Nomsa. Pamene Nomsa anafika pamalo apa, anali woyonda ndipo anali kuoneka wamadandaulo.

2

Patapita ntawi ing'ono, Nomsa anankala na mpamvu ndipo anayamba kusebela na nyama zinzake.

3

Siku lina mumwezi wamene uyo, ndeke ya bakabaka inabwela pamalo apa.

4

Mukati munali ka njovu kamene banavinikila na bulangete.

Aka ka njovu kanali kuitanidwa Ndiwa.

5

Ndiwa, wamene anali bu bulangete, anali na masiku asanu.

Amene anali kusunga nyana anali kupasa Ndiwa mukaka mubotolo.

6

Siku lina pakati pa usiku, nyama zonse zinausidwa pamene kanyama zina lake Ambia kanafika.

7

Ambia anali na myezi zisanu.

Pamene anafika, anali wolema kwambili cifukwa ca ulendo wamene anayenda.

8

Ambia anali kanyama kamukosu utali kwambili.

Cifukwa ca utali mukosi, osunga nyama anali kunyamula botolo mumwamba popasa Ambia mukaka.

9

Nyama zamasiye zomaliza kufika mu mwezi uyu, zinali tubana twa nkalamu.

Tunyama utu tinali kuitanidwa Kopi, Kepi na Keji.

Utu tubana twa nkalamu tunali na njala kwambili.

10

Osunga nyama na antu ake otandizila akonda nyama zonse kwambili, pamozi na nyama zosanmvela.

11

Antu apamalo apa asebenza na mpamvu.

Aziwisisa kuti siku lina, nyama izi zizayamba kuzisunga zeka ndipo zizakabwelela musanga.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Osunga nyama pamalo posungila nyama zing'ono
Author - Ursula Nafula, Nina Orange
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Magriet Brink
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs