Uyu ni Palesa. Zina lake itantauza "maluwa" mucitundu ca kwao ciSetswana.
Kuseni Palesa anauza mutengo wa ma lalanje nati. "Iwe mutengo utipase ma lalanje yambili."
Palesa ayenda kusukulu. Munjila anati kwa uzu, "Iwe uzu ukule kwambili, ndipo usafe."
Palesa anona maluwa yali imilile. "Imwe maluwa, zikoma pa maonekedwe anu okongola."
Pa sukulu, Palesa anauza kamutengo nati. "Iwe kamutengo, umela matepo akulu-akulu kuti tiziwelengela mucinfwile cako."
Palesa anauza mupanda wamene unazungulila sukulu lake nati, "Kula nampamvu kucinjiliza antu oyipa kungena."
Pamene Palesa anabwelela ku nyumba, anayenda kuona mutenga wama lalanje, "Kodi ma lalanje ako apya?"
"Mhm! Malalanje akali abisi," anati Palesa. "Tizaonana mailo iwe mutengo wamalalanje," anakamba. "Kapena mailo uzankala na malalanje akupya!"