N'cifukwa ciyani Nita ali cogadama?
Roxana Bouwer
Sarah Bouwer

Nita ali cogadama mu mtengo. Tsitsi lake lalitali lafika pansi.

Mitengo, udzu ndi zinthu zina zonse zili cogadama.

1

Mapazi a Nita ali m'mwamba.

Navi mlongo wake akuyenda pansi, ndipo akuti, "Ndinakuonapo pano uli cogadama. Wakhalanso cogadama! N'cifukwa ciyani?"

2

Nita akuseweretsa mapazi ake m'mwamba. Iye akuyesa kubisala kumbuyo kwa tsitsi lake.

"N'covuta kucita mmene acitira anznga. Ine ndine wosiyana ndi ena onse."

3

Navi akugwira Nita padzanja. Iye akufuna kuti Nita amvetsetse. Awiriwo akukwera mu mtengo pamwamba pomwe Navi amakonda.

Kucokera pamwamba pamenepo, iwo akuona zinthu zambiri. Akuona ana aksewra pansi.

4

5

Ana amenewo ndi osiyana onse.

Abe ndi wonenepa.

6

Chichi ali ndi cibalima cofiira pa thupi lake.

7

Lala ndi wamtali kwambiri.

8

Bamubamu ndi womasuka kwa munthu aliyense.

9

Lulu akuwerenga mwakacetecete.

10

Tapenyani tsitsi loyangalala ya Freya.

11

Sidi amavala magalasi kulikonse kumene akupita.

12

Ndipo ine ndine wowonda. Ndipo inu ndinu inu. Munthu aliyense ndi wosiyana ndi mnzake.

Ife tonse tiyenera kukhala osiyana.

13

Tsopano Nita akumva bwino cifukwa ca mnzake amene wapeza.

Kukhala cogadama si cinthu cabwino. Nita akusewera ndi anzake.

14
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
N'cifukwa ciyani Nita ali cogadama?
Author - Roxana Bouwer
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Sarah Bouwer
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs