Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo
Khothatso Ranoosi
Children of Paleng

Kalekale, Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo anali kuyambana.

1

Vuto linali loti Dzuwa linali kufuna kuwala nthawi iliyonse. Mwezi unali kufuna kuwala masiku onse.

Mvula inali kufuna kugwa masiku onse. Ndiponso Mphepo inali kufuna kuwomba nthawi zonse.

2

Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo zinagwirizana kuti zikambirane. Dzuwa linafunsa Mwezi kuti, "Kodi umagwira nchito yotani yothandiza dziko?"

Mwezi unati, "Ine ndimawala usiku kuti nyama zizipeza cakudya."

3

Mwezi unafunsa Mvula nuti, "Kodi umagwira nchito yotani yothandiza dziko?"

Mvula inati, "Ine ndimapatsa dziko madzi kuti mitengo ndi maluwa zizikula. Ndipo ndimapereka madzi akumwa kunyama."

4

Mvula inafunsa Mphepo niiti, "Kodi umagwira nchito yotani kuthandiza dziko?"

Mphepo inati, "Ine ndimapsera dziko. Ndiponso ndimamwazamwaza mvula pa dziko lonse."

5

Mphepo inafunsa Dzuwa niiti, "Kodi umagwira nchito yotani kuthandiza dziko?"

Dzuwa linyayankha niiti, "Ine ndipatsa dziko kuwala ndiponso ndi ndimafunditsa dziko lapansi kuti nyama ndi mitengo zikhale ndi moyo."

6

Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo zinamvera zonena za wina ndi mnzake mwacidwi.

7

Dzuwa linati, "Taonani kuti ife tonse timathandiza dziko lapansi m'njira zathu zosiyanasiyana."

"Inde. Kulibe wina aliyense mwa ife amene amapambana mnzake," unatero Mwezi.

"Tiyenera kugwirira nchito pamodzi," inatero Mvula. Mphepo inati, "Ndicabwino kuti tonsefe tigawane masiku."

8

Cimeneci ndiye cifukwa caka nthawi zina timaona mwezi pamene kuli dzuwa. Ndipo timamva mphepo pamene kuli mvula.

Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo zimagwirizana kugwirira nchito pamodzi.

9

Kodi iwe umakonda dzuwa, mwezi, mvula kapena mphepo?

Lemba cimene umakonda.

10

Zuba, mwezi, mvula na mpepo zigwila ncito pamozi kutandiza ziko. Kodi iwe umagwila ncito yotani kutandizila ziko?

11
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Dzuwa, Mwezi, Mvula ndi Mphepo
Author - Khothatso Ranoosi
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Children of Paleng
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs