Nthano ya nyemba
Nina Orange
Nina Orange

Mnzanga anandipatsa njere za nyemba kucokera m'munda wake.

1

Ndinabzala nyemba zija m'nthaka.

2

Nyemba zinamere kucokera m'nthaka.

3

M'mera unakula ukupenya kudzuwa.

Mizu imera kulowa pansi m'nthaka.

4

M'mera pokula umatuluka pamwamba panthaka.

5

M'mera umayamba kukula.

6

…ndi kukula.

7

Ndibzalanso nyemba zambiri.

8

Nyemba zikukula.

9

…ndi kukula.

10

Nyemba zamera makoko.

11

Nyemba zamera kupita pamwamba, ndi pamwamba, kukwera cipupa canga!

12

Ndimakolola makoko akauma.

13

Ndimacotsa nyemba m'makoko.

14

Ndimaphika nyemba, kuphikira pamodzi anyenzi ndi zokometsera.

15

Izi nyemba zapya kuti tidye.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nthano ya nyemba
Author - Nina Orange
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Nina Orange
Language - CiNyanja
Level - First words