Daisy Wodabwitsa
Nozizwe Herero
Siya Masuku

Kalekale pafamu pena panali mudzi wina waung'ono.

1

Panali kukhala kankhuku kakang'ono kochedwa kuti Daisy.

2

"Ine ndikakula, ndifuna kuuluka m'mwamba, m'mwambamu mlengalenga," anatero Daisy.

3

Koma nkhuku zonse zinamuseka iye.

4

"Iwe ndiwe wosokonezeka," iwo anatero. "Ife sitidzasewera nawenso."

5

"Daisy, ife tonse tingapukuse mapiko athu, koma ndicovuta kwambiri kuti nkhuku ziuluke," Amai ake anamuuza.

6

Koma Daisy sanaleke kuyesa. Tsiku lililonse amayeserera payekha, kupukusa mapiko ake.

Puku, puku, puku, anapukusa mapiko ake koma sanakwanitse kuuluka.

7

Pamene anali kuyesetsa, anayerekezera kuti anali kuuluka mu mlengalenga ndi kupenya nkhuku pansi.

Iye anaganiza kuti amauluka pamwamba kuposa mpheta. "Taonani!" Mbalame zinatero, "Nkhuku imene ikuuluka!"

8

Conco, tsiku lililonse Daisy amapukusa mapiko ake, puku, puku, puku.

9

Iye amati akakwanitsa kunyamuka anali kugwera pansi.

10

"Sindidzakwanitsa kuuluka!" Daisy anadandaulira amai ake. Anzanga ena onse akunena zoona.

11

"Daisy, ndiwe wosiyana ndi nkhuku zina. Izo sizifuna kuuluka, koma iwe ufuna kuuluka! Iwe ungakwanitse kuuluka," anatero amai ake.

12

Tsiku lotsatira Daisy anakwera pamwamba pa khola ndipo anayamba kupusa mapiko ake puku, puku, puku ndipo anapukusabe mapiko ake ndipo potsirizira pake…

13

PHWEE…

14

Nkhuku zina zonse zinaseka kwambiri. "Ha,ha, ha! Tinakuuza! Nkhuku sizingauluke!"

15

Koma tsiku lotsatira, Daisy anakwera pamwamba kwambiri, pamwamb panyumba.

Puku, puku, puku, Daisy anapukusa mapiko ake.

16

Iye anauluka m'mwamba ndi kupukusa mapiko ndi kupukusa mapiko ndipo potstira pake…..

17

Iye anapitiriza kuuluka! Mpweya pansi pa mapiko ake unakula ndipo anauluka m'mwamba ndi m'mwamba! Mpheta ndi anamzeze anati, "Codabwitsa! Nkhuku ikuuluka!"

18

Ndipo nkhuku zina zinafuna kukhala ngati Daisy.

19

Nkhuku zinati, "Taonani Daisy ndiwe wodabwitsa!"

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Daisy Wodabwitsa
Author - Nozizwe Herero
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Siya Masuku
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs