Mfumu ya M'mawa Okha
Nazinomwe Reading Group
AI Gemini

M'mawa, tambala amagwedeza mutu wake.

Kenako amakutumula mapiko ake.

1

Tambala amalira, kokoliko! Kokolikooo!

Phokoso limamveka mudzi onse.

2

Misoti ndi anapiye zonse zimadzuka.

Anthu nawonso amadzidzimuka mtulo.

3

Anthu nawonso amadzuka.

Abambo anyamula makasu.

Amayi ayamba kuphika chakudya cha mmawa.

4

Ana asukulu ayamba kukonzekera kupita kusukulu.

Mudzi onse uyamba ntchito za tsikulo.

5

Tambala aliranso kachiwiri.

Kudzutsa alesi onse okonda tulo.

6

Tambala ndi mfumu ya mudzi onse.

Imadzutsa aliyense.

7

Tsoka ilo, akalira masana palibe amalabada.

Ndi mfumu ya mmawa okha.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mfumu ya M'mawa Okha
Author - Nazinomwe Reading Group
Illustration - AI Gemini
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs