

Njaliwe adali kukhala ku Namwera. Iye ndi nzake, Ada, amakonda kusewera limodzi. Masewera awo adali phada, jingo ndi chibisalirano. Pa uwiri wawo, atsikanawa adali okondwa ndipo kulikonse amakhala ali limodzi.
Tsiku lina Ada sadabwere kuzasewera ndi Njaliwe ndipo iye adali ofunitsitsa kusewera.
"Ababa, Adatu sakubwera, bwanji lero ndisewereko mpira ndi anyamatawa?" Njaliwe adafunsa abambo ake.
"Ayi, sungasewere ndi awo, mpira ndi wa anyamata."
Njaliwe adayamba kulira. Anyamata aja adasiya kusewera mpira uja. Onse adali odabwa kuli mtsikanayo adali kufuna kusewera nawo mpira. "Sungathe kuthamanga iwe," mnyamata wina adatero. "Komanso tikugwetsa," iye adapitilira kuyankhula.
Njaliwe adathamanga. Iye adayamba kukwera mtengo. Aliyense adali ndi mantha kuti mtsikanayu akhoza kugwa mu mtengomo kapena kulumidwa ndi mavu kapena njoka. "Ine ndi mtsikana koma nditha kusewera mpira, nditha kukwera mu mtengo, ndi ndi..."
Njaliwe adakwerabe mtengowo ndipo adafika patali.
"Iwe Njaliwe, chonde tsika. Sukuyenera kusewera ndi anyamata ngakhale wakwera mu mtengo!" mayi ake adatero.
"Nde sinditsika. Ndigwe chabwino." Adatero Njaliwe.
"Njaliwe mwana wanga, tatsika. Tiye ku msika tikagule zitumbuwa." Adatero bambo ake.
"Ndilibe osewera naye, ndisiyeni. Nditsika Ada akabwera." Njaliwe adakanitsitsa.
Patadutsa kanthawi, Ada anatulukira. "Njaliwe, ndabweratu. Tsika tikasewere." Adatero Ada.
"Ada, unali kuti? Akundikaniza kusewera mpira ine, sinditsika! Ukalola kuti tiyambitse timu yathu ya mpira nditsika," adatero Njaliwe.
"Eya tsika, abambo ako akuti atigulira mpira wathu, tipeza atsikana ena, tipanga timu yathu," adatero Ada.
Njaliwe adatsika mu mtengo muja ndipo adali okondwera kuti mnzake wabwera komanso kuti ayambitsa timu yampira wamiyendo ya atsikana.

