

Kumadzulo kwa phiri la Dzalanyama kuli mudzi wotchuka komwe anthu adaona malodza chaka china. Makewana yemwe adali kukhala m'mudziwu adanenetsa kuti sapemphera kwa Chauta kuti apereke mvula chifukwa nyumba yake inali yosakonza denga.
"Mvula ikabwera, ndidzagona bwanji muno?" Adadandaula Makewana.
"Ine ndimagwetsa mvula, anthu amakolola zakudya zawo ndi kumasangalala, palibe yemwe amandikumbuka," anapitirira kudandaula.
"Chaka chino mufa ndi njala, tiona kuti mutani."
"Mwatani agogo mukungodziyankhulira nokha?"
Makewana adali odabwa kuona mtsikana wamapiko ataima pakhomo la nyumba yawo.
"Iwe ndi ndani? Wachokera kuti? Mayi ako ndi ndani?"
"Agogo, dekhani, ndikufuna ndimvetse dandaulo lanu."
"Usakhale ngati sukuwona wekha. Iyi nyumba. Chaka chino ndigonenso munomu?"
Makewana anafotokoza nkhawa yake. Iye adanenetsa kuti sakuona chifukwa choitanira mvula.
"Koma agogo, anthutu afa ndi njalatu. Taganizirani ana a m'mudzi muno.
Mtsikanayo anawomba m'manja ndipo nyumbayo idasintha maonekedwe. Munabwera mpando ndi kabedi ndipo denga lake linali lamalata komanso losamveka phokoso kukamagwa mvula. Ataombanso m'manja, munawala magetsi. Koma Makewana sanaokondwe nazo.
"Iwe mtsikana, wabwera kuzandiyesa eti. Inetu ndi Makewana. Ana anga akabwera adzagona patipo apa?"
"Ayi agogo sindikukuyesani. Tadikirani." Mtsikanayo adaombanso m'manja ndipo nyumbayo inakula.
"Eeeh taonani! Iwe mtsikana uli kuti? Awa nde ndi malodza ndithu. Ineyo Makewana, nyumba yonseyi yanga?" Makewana adaomba m'manja kuti phu. "Ine ndathokoza mtsikana, ndipemphenso china tabwera."
"Ayi agogo. Ndizosatheka kukupatsani zinthu ziwiri pakamodzi. Ndibweranso chaka chamawa ndidzakuthandizani zinazo. Apa pitani ku kachisi mukapereke nsembe kuti mvula ibwere, anthu adzale chimanga."
"Zikomo kwambiri," Makewana anathokoza.

