Kusamvera kunandimanitsa zabwino
Mustafa Bunaya
AI Gemini

Ndine Chikondi. Ndimakhala kufupi ndi nyanja ya Malawi.

Nyanjayi ndi yaikulu komanso yokongola kwambiri.

1

Kalekale anzanga akamapita kusukulu, ine ndinkathamangira kunyanja.

Ndimathamangira kunyanja koona asodzi akuwedza nsomba uku ndikulingalira zokasewera mpira masana ake.

2

Mayi anga sankasangalala ndi mchitidwewu. "Chikondi, tabwera! Uchedwa kusukulu." Iwo anakalipa tsiku lina.

Ndipo ndinayankha, "Ndikubwera ndatsala pang'ono."

Koma sindinapite, ndinali ndikulingalira zogoletsa zigoli kumpira masana ake.

3

Tsiku lina kunyanja kuja kunabwera woimba wotchuka.

Ana onse anamuthamangira chifukwa amapereka mphatso kwa ana omwe amuonetsa ntchito yomwe achita kusukulu.

4

"Ndionetseni kaye zomwe mwapanga kusukulu ndipo ndikupatsani mipira," anatero woyimbayo uku akusekerera.

Ndinalibe ntchito yakusukulu yoti ndingamuonetse choncho sindinapeze nawo mpira.

5

Anzanga anapeza mipira yosewerera masewera a mpira wa miyendo koma ine sindinapeze kanthu.

Ndinakhala mphepete mwa nyanja uku nditakhumudwa.

6

Ndinakumbukira zomwe amama amanena mobwerezabwereza. "Kusamvera kumamanitsa zabwino."

Tsopano ndimapita kusukulu nthawi zonse ndisanapite kunyanja koona nsomba kapena kosewera mpira.

7

Ndimakaonabe nsomba zikudumpha, koma ndimayamba ndagwira ntchito yakusukulu kaye.

Kumvera amama ndi kwabwino. Nthawi zina umatha kupeza nazo mpira.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kusamvera kunandimanitsa zabwino
Author - Mustafa Bunaya
Illustration - AI Gemini
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs