Mlimi
Asiatu Kandewu
Patience Khama

Nthawi zonse amalawira kumunda.

Iye amalima mbewu zosiyanasiyana.

1

Pochoka kumunda amabwera ndi zakudya zosiyanasiyana.

Izi amakapatsa banja lake kuti lidye

2

Lero wagula mlamba.

Iye akuyimba mluzu pamene akubwerera kunyumba

3

Mlamba ndi ndiwo yabwino.

Mlamba umakoma komanso umatipatsa ma vitameni kuti tizikula bwino.

4

Atafika kunyumba, mlimiyu wapeza mwana wake akulira.

Mwanayo atonthola ataona bambo ake atanyamula mlambawo.

5

Banja lonse likusangalala poti lidyera mlambawo

6
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mlimi
Author - Asiatu Kandewu
Illustration - Patience Khama, Catherine Groenewald
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs