Tsiku Lina, ndidzachoka m'mudzi muno. Ndizikakhala ndi kugwira ntchito kutawuni.
Ndidzapita ku sekondale sukulu kenako ku yunivesite ya ku Zomba.
Kuyunivesite ndikaphunzira za zachuma.
Ndidzafunsira ntchito ku banki.
Ndidzakhala mkulu wa banki.
Ndizidzakumana ndi mabwana a makampani osiyanasiyana. Ndizidzawapatsa ngongole.
Ndidzayendetsa galimoto yayikulu.
Ndidzayenda m’mayiko ambiri.
Ndikutha kuona nditavala suti.
Ndidzakwaniritsa izi polimbikira sukulu tsiku ndi tsiku.