Nkhalango ya zipatso za mtchire
Nazinomwe ASb Reading Group
Offei Tettey Eugene

Beni amakhala ku tawuni.

Wabwera kumudzi kudzacheza ndi agogo.

1

Agogo a Beni ali ndi nkhalango ya zipatso za mtchire.

"Lero ndikuonetsa zipatso za mtchire," Agogo anamuuza Beni.

2

Uwu ndi mtengo wa nthudza.

Nthudza zaziwisi zimachita khambi, zakupsa zimazuna. Mtengo wake ndi wa minga.

3

Awa ndi masuku.

Amakoma akapsa, awisi amachita khambi.

4

Awa ndi matowo. Timatafuna ngati chingamu.

Amazuna ngati muli shuga.

5

Mtengo uwu ndi wa chimanga cha chizungu.

Mkati mwa chipatso mumakhala chimanga chofiira.

6

Uwu ndi mtengo wa mpoza.

Samala osakwera, mpoza suchedwa kuthyoka.

7

Uyu ndi katope.

Mulibe zipatso, nthawi yake siinakwane.

8

Uyu ndi bwemba.

Bwemba umawawasa.

9

Beni, ndatopa kuyenda. Tipitiliza mawa.

Ndakuonetsa zipatso zingati?

10
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkhalango ya zipatso za mtchire
Author - Nazinomwe ASb Reading Group
Illustration - Offei Tettey Eugene
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs