

Kale - kale nthawi ina zaka Zapita, Mvula sinagwe bwino ndipo madzi anabvuta cakaco.
Cifukwa ca kusowa kwa madzi, nyama zonse zinabvutika kwambiri komanso nyama zina zinafa ndi ludzu.
Mfumu mkango anaitanitsa msonkhano. M'mawa mwake nthawi itakwana 2 koloko m'madzulo nyama zonse zosiyana-siyana zinakumana kwa mdumu mkango.
Ndipo mfumu mkango analandila nyama zonse naziuza kuti zikhale zomasuka kufotokoza maganizo awo.
Mfumu mkango inati kunyama zinzake, ndibwino kuti tikafukule madzi ku dambo, cifukwa tikapanda kutero anzanganu tikutha tonse kufa ndi ludzu.
Zimvekere nyama zonse Inde mfumu, ayo ndi maganizo abwino kwambiri.
Mfumu mkango inalamulira anzake.
Kutaca tsiku lotsatira m'mawa, nyama zonse zinakumana kudambo ndikuyamba kufukula citsime ca madzi, citsime cinabvuta kukumba cifukwa madzi anali patali.
Koma nyamazo zinalimbikira ndipo zinapeza madzi. Kucitsimeko anaikako malonda.
Kalulu anakana kukumbako madzi. Koma atamva Kuti madzi apezeka, anapita kukatunga madzi koma anapezako gulu ndipo anamuuwa kotero kalulu anathawa.
Kalulu anakalipa kwambiri.
M'mawa mwake, kalulu anapha nkhuku natengako mabonzo kuti akapatse gulu kuti iye atungeko madzi.
Atafika anauza galu Kuti anali ndi malonda. Galu Poona kuti yanali mafupa anagonjeka nati kalulu asambe ndi kutunga madzi.
Kalulu anapitanso kuti akamwe madzi koma anapezako kaingo.kalulu anabwelera ndi kupita kukafuna uci. Ataupeza anapitanso kumadzi ndikuuza kaingo Kuti iye anali kugulitsa uci. Kaingo anagonjera nalola kalulu kuti atunge madzi.
Nyama zonse zinabvutika mtima.koma fulu ananena pulani yake nati ampake phula kuti ngati kalulu wabwera akalamatile ndipo nyama zonse zikamupeza kalulu. Nyama zonse zinabvomera ndi ganizo ya fulu niziti inali ganizo yopambana.
Mwanthawi zonse,kalulu anapanga ulendo wopita kumadzi atanyamula uci.Atafika kumadzi kunali zii. Anapenya -penya koma kunalibe aliyense. Kalulu anayamba kusamba ndipo atamaliza anaganiza zokhala pamadzi .
Kalulu anadabwa cifukwa analephera kuimilira.Anayesa kukuwa Kuti mwala umuleke koma zinabvuta, Anayesa kumenya khofi koma dzanja inalamatila. Anaponya cibakha mendo nayonso yanalamatila, anayesanso mphuno koma mphunonso nayo inalamatila.
Zitabwera nyama zonse, zinapeza kalulu ali olamatila. Nyama zonse zija zinapangana zakupha kalulu. Kalulu atamva tero anauza nyama kuti mukandipanditsira pa ciputu ndidzafa koma mukandipanditsira pa mwala mwayi wanga tidiii.
Nyama zija zinamva pulani ya kalulu ndipo anamupanditsira pa ciputu ndipo kalulu anathawa.
Mau olimba mnkhani:
Musonkhano
Anagonjera
Pulano
Ulendo

