

Pamudzi wina wodziwika kuti Kachingwe, panali Abambo ndi Amai.
Anthu awiriwa anali atakwatilana. Anakhala zaka zisanu paukwati koma osaona cipatso.
Mkupita Kwa nthawi, Mulungu anawapasa mphatso yakukhala ndi ana awiri amphundu. Maina awo anali Yohane ndi Malita.
Patapita zaka zitatu, mai wa ana awa anamwalila. Ana awa anakhala ndi bambo okha Kwa caka cimodzi.
Bambo Yeketani anaganiza zokwatila mkazi wina kuti aziwathandiza kusunga ana. Mwa mwai wanji anapeza amai wokongola kwambiri ndipo anamanga naye banja.
Patapita masiku wocepa, amai awo anayamba kuzonda ana amuna awo aja Yohane ndi Malita. Cifukwa cowazondera ndi cikondi comwe anali kulandila kuli mbambo wao.
Tsiku Lina Bambo Yeketani anapita Ku nchito. Akazi awo anaona kuti ndiye m'pata wakuti aonetse cipongwe Kwa ana aja.
Amai awo anapita kuseli Kwa nyumba ndikukumba dzenje lalitali. Atatha kukumba, kumwamba kunacita mudima wamvula. Amai awo anauza ana aja kuti alowe kudzenje lomwe anakumba cifukwa mvula izagwetsa manyumba.
Ana aja anathamanga ndi kukalowa kudzenje ija. Amai aja anatenga ciweye ca lilata ndi kuika pamwamba ndiponso anafocelapo ndi dothi.
Pomwe Bambo Yeketani anafika, anafunsa akazi awo, 'Make Kodi ana anthu mwati acoma bwino? Nanga alikuti?' Amai aja mowuma mutima anati, 'apita kukasewera abwera.' Bambo aja anati zikomo.
Bambo Yeketani atalandila cakudya cam'mdzulo anapita mucipinda cawo cogonamo. Iwo anagona tulo tofanato cifukwa anali atalema kwambiri.
M'mawa kutacha, anaona kuti anawo panyumba panalibe. Ici cinawakhumudwitsa kwambiri. Anayamba kufuna funa. Atazungulila kuseli Kwa nyumba anaona dothi lofuila ndipo anadabwa nati, Kodi iwe make Yohane cinafukula apa ndi ciani?
Amai anati 'Kaya sindiziwa.' Pakupenyetsetsa anawona ciweye ca lata ndipo anafukulapo. Atasizila mkati anaona kuti muli Yohane ndi Malita.
Bambo Yeketani analowa mdzenje ndi kutulutsa ana awo. Akazi awo anakhumata kwambiri. Bambo Yeketani anafunsa anawo pazomwe zinacitika ndipo ana analankhula zonse anawauza amai ao opeza aja.
Bambo anakalipa kwambiri kotero kuti anaudza akazi ao kuti alonge katundu wao ndi kupita kwao. Anawauza kuti ndiwe munthu woipa mtima kwambiri. Tero banja la a Yeketani ndi akazi ao aciwiri linathera pompo.
Tsopano yesani kukumbukila ndi kuyankha mafunso awa pa zomwe mwawerenga munkhani iyi
1. Culani dzina la Bambo omwe anveka munkhani iyi........................
2. Kodi abambo awa anali ndi ana angati.......
3. Abambo anakhala zaka zingati paukwati osaona cipatso?
4. Kodi akazi aciwiri anacita coipa cotani Ku ana?.........................
5. Nanga cikwati cao caciwiri cinacitika cotani.....
6. Kodi mwaphunzirapo ciyani pankhani imeneyi?

