ZINCHITO ZA NKHUKU
Impact Network Peter Langdon Phiri

Dzina langa ndine nkhuku.

1

Ana anga achedwa anapiyo.

2

Ndili ndi zinchito zambiri.

3

Ndimakhala ndi ma zira.

4

Anthu amadya kapena kugulitsa ma zira anga.

5

Anthu ambiri amandipanga ndiwo cifukwa ndili ndi nyama yabwino kwambiri.

6

Komanso ndili ndi nchito youtsa anthu cifukwa za nthawi ndimazisata bwino kwambiri.

7

Pazinthu zonse za padziko lapansi pano, mdani wanga ndi mpeni.

8

KEY WORDS TRANSLATION

1. Nchito............. work
2. Nkhuku........... Chicken
3. Anapiyo.......... Chicks
4. Mazira.......... Eggs
5. Nyama............ Meat
6. Mdani............. Enemy
7. Mpeni............. Knife

9
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
ZINCHITO ZA NKHUKU
Author - Impact Network Peter Langdon Phiri
Illustration -
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs